Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April: May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! June: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, kapena buku lililonse la masamba 192.
◼ Ofalitsa amene akufuna kukhala apainiya othandiza mu April ndi m’May angakonzekere tsopano lino nkupereka mafomu awo msanga. Zimenezo zidzathandiza akulu kukonzekera utumiki wakumunda ndi kupeza magazini ndi mabuku ena okwanira. Maina a anthu ovomerezedwa kukhala apainiya othandiza muwalengeze kumpingo.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina yemwe wamsankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa March 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detilo. Mutatsiriza zimenezo lengezani kumpingo.
◼ Amene akugwirizana ndi mpingo azitumiza masabusikripishoni a Nsanja ya Olonda ndi a Galamukani! atsopano ndi okonzanso, kuphatikizapo masabusikripishoni awoawo, kudzera mumpingo.
◼ Sosaite siimadzazira wofalitsa fomu yoodera mabuku. Woyang’anira wotsogoza aziona kuti mwezi uliwonse mpingo usanatumize ku Sosaite fomu yoodera mabuku, pazikhala chilengezo kuti onse amene akufuna kuoda mabuku awoawo aziuza mbale wosamalira mabuku. Chonde muzikumbukira kuti ndi mabuku ati ofuna oda yapadera.
◼ Tangoti tikumbutse mipingo kuti muzitumiza ku Sosaite malipoti a Utumiki Wakumunda a Mpingo (S-1-CN) pomafika pa 6 mwezi wanawo. Mipingo yambiri imadikira galimoto ya Sosaite kudzatenga malipoti, koma zimenezo zimatichedwetsa kwambiri kutumiza malipoti ku Bungwe Lolamulira panthaŵi yabwino. Tikukhulupirira kuti mudzaona kuti nkofunika kuchitadi changu pankhani imeneyi kuti tisamachedwe kutumiza lipoti lolondola.
◼ Brosha lakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? lidzaphunziridwa pa maphunziro a buku a mpingo kuyambira pa May 4. Mipingo yomwe ikuwafuna ambiri ingaode msanga.
◼ Chipinda cha Mabuku cha Sosaite mu Lilongwe chisamutsidwira ku Area 12, Plot 7. Chizitsegudwabe Lolemba ndi Lachisanu.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zomwe Zilipo:
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo—Chingelezi
Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—Chingelezi
Comprehensive Concordance—Chingelezi
Imbirani Yehova Zitamando (Laling’ono)—Chingelezi
Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kodi Ingakuvulazeni? Kodi Ilikodi?—Chicheŵa, Chingelezi
Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira—Chingelezi
◼ Makaseti Atsopano Omwe Alipo:
Why Respect Theocratic Arrangement?—Chingelezi