Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/98 tsamba 3-4
  • Kulemba Lipoti la Nthaŵi ya Utumiki Wathu Wakumunda Molondola

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulemba Lipoti la Nthaŵi ya Utumiki Wathu Wakumunda Molondola
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 4/98 tsamba 3-4

Kulemba Lipoti la Nthaŵi ya Utumiki Wathu Wakumunda Molondola

1 Nzosangalatsa kudziŵa kuti Yehova nthaŵi zonse wasunga mbiri ya ntchito za atumiki ake okhulupirika. Analemba chiŵerengero cha masiku amene Nowa anakhala m’chingalaŵa ndi zaka zomwe Aisrayeli anayenda m’chipululu. Mulungu anasunga chiŵerengero cha amene anali okhulupirika ndiponso amene anali osamvera. Anauzira mbiri yolembedwa imeneyi ya zimene zinachitika, akumatiuza bwino mmene iye amaonera kulemba malipoti ndi kusunga mbiri yolondola.—Gen. 46:27; Eks. 12:37; Ower. 7:7; 2 Maf. 19:35; Mac. 2:41; 19:19.

2 Malipoti athu a nthaŵi imene timawononga mwezi ndi mwezi mu utumiki wakumunda alinso ofunika kwambiri. Chonde ŵerengani mafunso otsatira ndi mayankho ake bwinobwino, kuti akuthandizeni kudziŵa mmene mungaŵerengere nthaŵi ya utumiki wanu molondola kwambiri.

◼ Kodi ndi liti pamene tingayambe kuŵerenga nthaŵi ya ulaliki wathu?

 Kuchokera panthaŵi imene tafika panyumba yoyamba kapena kupanga ulendo wathu wobwereza woyamba, ngakhale ngati palibe munthu panyumba. Buku la Uminisitala Wathu (om-CN), tsamba 104, ndime 1, limati: “Nthaŵi yanu yautumiki wakumunda iyenera kuyamba pamene inu muyamba ntchito yanu yaumboni ndi kutha pamene inu mutsiriza nyumba yanu yotsiriza.”

◼ Kodi tingaŵerengere nthaŵi pamene tikuyenda kuchoka panyumba ina kumka pa yotsatira ndi paphunziro lina la Baibulo kumka pa lotsatira?

 Inde. Imeneyi ili mbali ya utumiki wathu, tili m’munda wa Yehova. Ngati taima pakantini kapena panyumba ya mbale kuti timwe zoziziritsa kukhosi, pamenepo sitiyenera kuŵerengera nthaŵiyo, pakuti sitilinso mu utumiki wakumunda.

◼ Kodi tingaŵerengere nthaŵi yathu popita ndi pobwerako ku utumiki wakumunda?

 Nthaŵi yathu ya utumiki imayamba pamene tayamba ntchito yathu ya umboni. Ngati popita ku gawo lathu tilalikira kapena kugaŵira trakiti kwa wina wake, ndiye kuti tidzayambira pamenepo kuŵerenga nthaŵi yathu. Ngati tachoka m’gawo lathu tikupita kunyumba ndipo tipitirizabe kuchitira umboni kwa anthu kapena kuwagaŵira matrakiti pamene tikuyenda, pamenepo tiyenera kuŵerengera nthaŵi kufikira titalankhula ndi munthu womaliza. Komabe, ngati sitilalikira popita ku gawo kapena pobwerako, tiyenera kungoŵerengera nthaŵi imene tawononga kuchokera panyumba yoyamba kufikapo m’gawo lathu mpaka nyumba yomaliza, ngakhale ngati sitinapezepo aliyense panyumba.

◼ Kodi tingaŵerengere nthaŵi ya umboni wamwamwaŵi?

 Inde. Sosaite imafuna kudziŵa za nthaŵi imene yawonongedwa kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu. Umboni wamwamwaŵi ngwofunika kwambiri pantchito imeneyi choncho nthaŵiyo iyenera kuŵerengedwa. Khalani ndi fomu ya malipoti pafupi, ndipo lembani kuseri kwake nthaŵi yonse imene mwawonongera pa umboni wamwamwaŵi, ngakhale ngati zili mphindi zisanu kapena khumi. Mutaziwonkhetsa pamapeto pa mwezi, mungadabwe kupeza kuti zikukwana ola limodzi kapena aŵiri. Komatu, maola athunthu ndiwo ayenera kulembedwa pa malipoti athu. Mutakhala ndi mphindi 15 kapena theka la ola lotsalira, pamenepo muyenera kuliika pa lipoti lanu la mwezi wotsatira. Ngati wofalitsa aliyense angachite ola limodzi mu umboni wamwamwaŵi pamwezi, limenelo lingafike pa chiwonkhetso cha maola 42,000. Koma ngati aliyense anyalanyaza kulemba mphindi zowonongedwa apa ndi apo mu umboni wamwamwaŵi, nthaŵi yonse ya umboni wowonjezera umenewu simaŵerengeredwa. Buku la Uminisitala Wathu (om-CN), tsamba 103, ndime 2, limati: “Nkofunika kupanga lipoti lolongosoka.”

◼ Ngati tafika panyumba kuti tichititse phunziro la Baibulo ndiye tapeza palibe munthu, kodi nthaŵi yolalikira iyenera kuŵerengeredwa?

 Ngati ndi panyumba yokhayo imene tafikapo, ndipo sitinachitire umboni popita kumeneko kapena pobwerera kunyumba kwathu, ndiye kuti sitiyenera kuŵerengera nthaŵi iliyonse. Ndipo sitiyenera kuŵerengeranso ulendo wobwereza. Komabe, ngati tayamba kale utumiki wathu wakumunda kwa munthu wina kapena phunziro, koma nkupeza kuti phunziro linalo palibe panyumba, tidzaŵerengera nthaŵi yathu chifukwa tayamba kale utumiki wathu. Ndiye tidzapitiriza kuŵerengera nthaŵi yathu mpaka titafika panyumba yomaliza ngakhale ngati sitipezapo munthu.

◼ Kodi makolo angaŵerengere nthaŵi yawo, ulendo wobwereza ndi phunziro la Baibulo, pamene akuphunzitsa ana awo?

 Inde. Ngati ana ali osabatizidwa, angaŵerengere nthaŵiyo mpaka ola limodzi pamlungu, ulendo umodzi wobwereza paphunziro lililonse ndi phunziro la Baibulo limodzi pamapeto pa mwezi. Onani buku la Uminisitala Wathu (om-CN), masamba 103 ndi 104.

◼ Kodi mbale amene akukamba nkhani yapoyera angaŵerengere nthaŵiyo monga ulaliki?

 Inde. Koma nkhani zapoyera zokha, osati nkhani za Msonkhano Wautumiki, Sukulu Yautumiki Wateokratiki, kuchititsa misonkhano kapena Maphunziro a Buku a Mpingo.

◼ Ngati abale kapena alongo aŵiri apezeka paphunziro la Baibulo limodzi, kodi aŵiriwo angaŵerengere nthaŵi yawo, ulendo wobwereza ndi phunziro la Baibulo?

 Onse aŵiri angaŵerengere nthaŵi ya ulaliki, malinga ngati aŵiriwo akutenga nawo mbali mokangalika kuphunzitsa. Mmodzi yekha ndiye ayenera kuŵerengera ulendo wobwereza nthaŵi iliyonse ndi phunziro la Baibulo limodzi pamapeto pa mwezi. Sosaite simalimbikitsa kuti anthu oposa pa aŵiri alalikire limodzi. Chotero, ngati anthu oposa aŵiri apita mu utumiki ndi kugwira ntchito limodzi, kapena ngati oposa aŵiri apitira limodzi kukachititsa phunziro la Baibulo, pamenepo aŵiri okha ndiwo ayenera kuŵerengera nthaŵi.

◼ Kodi ndi liti pamene tingaŵerengere ulendo wobwereza?

 Kuti tiŵerengere ulendo wobwereza, tiyenera kuonana ndi munthu mmodzimodzi amene tinachitirako umboni poyamba. Ziyeneranso kukhala choncho ngakhale ngati munthu ameneyo ali wotanganitsidwa ndipo sangathe kutilandira, kapena atiuza kuti sakufunanso. Tapanga ulendo wobwereza ndipo tampeza panyumba; cholinga chathu chinali kukulitsa chidwi chake. Ngati ali wotanganitsidwa kwambiri kapena safunanso kuphunzira, si mlandu wathu; tachita mbali yathu mokhulupirika. Tingaŵerengere maulendo obwereza ndi nthaŵi ya utumiki wakumunda popereka magazini kwa amene timapitako kaŵirikaŵiri, pochitira umboni kachiŵiri kwa munthu mmodzimodzi pafoni, kapena polembera kalata wina wake amene analalikidwapo kale. Ndiponso, tikafika panyumba ya munthu wochita chidwi kukamtenga kupita naye kumsonkhano, umenewo ndi ulendo wobwereza. Nthaŵi iliyonse imene tichita phunziro la Baibulo la panyumba tiyeneranso kuŵerengera ulendo wobwereza umodzi.

◼ Ngati mukuchititsa phunziro la Baibulo pali anthu atatu, kodi ndi maphunziro angati amene angawerengedwe, atatu kapena limodzi?

 Limodzi lokha. Sosaite imafuna kudziŵa chiŵerengero cha maphunziro amene anachitidwa osati unyinji wa anthu opezekapo. Popeza onse akuphunzitsidwa panthaŵi imodzi, ndi phunziro limodzi lokha la Baibulo la panyumba ndi ulendo wobwereza umodzi.

3 Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchitira lipoti ntchito ya utumiki wathu wakumunda mwezi ndi mwezi? Malipoti amatisangalatsa kwambiri ndipo amathandiza Sosaite kuona mmene ntchito ya padziko lonse ikupitira patsogolo. Zigamulo ziyenera kupangidwa ponena za kumene kufunikira thandizo kwambiri kapena mtundu wa mabuku ofunikira kupangidwa ndi unyinji wake. Akulu mumpingo uliwonse amagwiritsira ntchito malipoti a utumiki wakumunda pofuna kuona pamene pangafunikire kuwongolera. Malipoti abwino amalimbikitsa, kutisonkhezera tonsefe kupenda utumiki wathu kuona ngati pali pamene tingawongolere. Ofalitsa onse ayenera kuzindikira kuti ndi ntchito yawo aliyense payekha kupereka lipoti la utumiki wakumunda mwamsanga mwezi uliwonse.

4 Akulu ayenera kupitiriza kukumbutsa ndi kuthandiza abale kukonza malipoti awo mwezi ndi mwezi. Ayenera kuyesetsa ndithu kuthandiza amene akuyamba kumene kupita mu utumiki kuti amvetse mmene angalembere masilipi awo a malipoti. Mungapende limodzi nawo chidziŵitso chimene chili m’nkhani ino.

5 Kuthandizira Lipoti Kukhala Lolondola. Mlembi ayenera kuyesetsa ndithu kukonza lipoti la mpingo pafomu ya S-1 ndi kuitumiza mwamsanga ku Sosaite. Safunikira kuyembekezera kuti mpaka alandire lipoti kwa wofalitsa ndi mpainiya aliyense ngati zimenezo zidzachedwetsa kutumiza lipoti ku Sosaite. Mipingo ina imawonkhetsa malipoti a ofalitsa pamodzi ndi a apainiya. Ena amalemba malipoti a ofalitsa pamzera wa apainiya. Zimenezo zimasokoneza kwambiri. Pakhadi la lipoti la mpingo (S-1) pali mizera itatu. Woyamba uyenera kusonyeza chiŵerengero cha ofalitsa ndi chiwonkhetso cha utumiki wawo wakumunda. Wachiŵiri umasonyeza unyinji wa apainiya othandiza amene analipo mweziwo ndi chiwonkhetso cha utumiki wawo wakumunda. Mzera womaliza umasonyeza chiŵerengero cha apainiya okhazikika mumpingowo amene apereka lipoti ndiponso chiwonkhetso cha utumiki wawo wakumunda.

6 Malipoti ochedwa (S-4) mlembi adzawasunga ndipo adzawaphatikiza pa lipoti lotsatira limene adzatumiza ku Sosaite. Lipoti lililonse pa S-4 adzaliŵerengera kukhala wofalitsa mmodzi. Ngati mbale mmodzimodziyo wapereka malipoti aŵiri, lina lipoti lochedwa la mwezi wapitawo, adzamŵerengera kukhala ofalitsa aŵiri chifukwa wapereka malipoti aŵiri. Mwanjira imeneyi palibe wofalitsa amene adzasiyidwa.

7 Mlembi ayenera kupatsa wochititsa phunziro la buku aliyense mpambo wa ofalitsa onse m’kagulu kake amene sanapereke lipoti mweziwo. Iyenso angawathandize mwachikondi amenewo, ndipo angalandire malipoti kwa amene anaiŵala. Ayenera kuwayamikira abale kaamba ka utumiki wawo wakumunda ngakhale kuli kwakuti iwo amaiŵala kupereka malipoti.

8 Mipingo ina imalephera kupereka lipoti mwezi ndi mwezi ndipo imafunikira kukumbutsidwa. Mwachitsanzo, lipoti la October linasonyeza ofalitsa 40,014 amene ali m’Malaŵi. Kodi nchifukwa ninji chiŵerengero cha ofalitsa chinatsika kuposa miyezi yapitayo? Chifukwa chakuti mipingo 556 pa mipingo 589 inatumiza malipoti awo ku Sosaite mweziwo. Zimenezo zikutanthauza kuti mipingo 33 inaiŵala ndipo inafunikira kukumbutsidwa.

9 Tikhulupirira kuti mafotokozedwe ameneŵa omveketsa bwino mmene tingaŵerengere nthaŵi ya utumiki wakumunda adzathandizira kulemba lipoti lolondola kwambiri ndipo zimenezo zidzapereka chithunzi chenicheni ponena za nthaŵi imene timawonongera mu utumiki wakumunda kutamanda Yehova. Pokhala kuti zimenezi zamveketsedwa bwino, tiyeni tonsefe tionetsetse kuti sitikuiŵala kupereka malipoti athu mwezi ndi mwezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena