Lakalakani Chakudya Chauzimu
1 Kodi mumalakalaka chakudya chauzimu? Kodi mukufunafuna mipata yowonjezera kumvetsetsa kwanu Malemba kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu, ndi kuti mukhale okonzekera bwino kuthandiza ena kupeza chidziŵitso cholongosoka cha choonadi? Kodi mumamva bwanji ngati tsiku ladutsa inu musanaganizireko zinthu zauzimu mozama? Kodi mumadzimva kuti mukusoŵa kenakake?
2 Sizimangochitika kuti tikumalakalakadi chakudya chauzimu. Tisanakhale ophunzira a Yesu Kristu, tingakhale kuti tinaloŵereradi m’zochitika zatsiku ndi tsiku ndi zokondweretsa zina. Mtumwi Petro analimbikitsa okhulupirira atsopano kuti: “Monga makanda obadwa chatsopano, kulitsani chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu.”—1 Pet. 2:2, NW.
3 Koma si achatsopano okha amene afunika kumalingalira za njala yawo yauzimu. (Aheb. 5:14–6:2) Monga mmene munthu amene akunyalanyaza chakudya chakuthupi sangayembekezere kuchita ntchito yabwino tsiku ndi tsiku, munthu sangakhalenso ndi chikhulupiriro cholimba nchosagwedera ngati sadzidyetsa mwauzimu. Popanda chakudya chauzimu choyenerera, munthu sangakhale wofunitsitsa kulengeza “uthenga wabwino.” Sizidzasefukira m’mtima mwake ndi kumpangitsa kulankhula.—Luka 6:45.
4 Mmene Munthu Angachitire Njala Yauzimu: Kodi tingachitenji kuti tikulitse njala yauzimu? Tikufunikira chinachake ndithu choti chitisonkhezere kufuna zinthu zauzimu. Nchimene mtumwi Petro anasonya pamene analemba kuti, “ngati mwalaŵa kuti Ambuye ali wokoma mtima.” (1 Pet. 2:3) Motero ngati muona kuti chikhumbo chanu cha chakudya chauzimu sichili mmene chiyenera kukhalira, ganizirani za zimene mwalaŵapo kale. Nthaŵi zonse kumalingalira za zinthu zimene talaŵapo kale kungakhudze mitima yathu ndi kutisonkhezera kusonyeza kuti timayamikira Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu.
5 Kodi mzimu woyamikira umenewu udzaonekera bwanji? Tidzafuna kumaphunzitsidwa ndi Yehova ndi Mwana wake. Zoonadi, pamafunika kuyesetsa kuti tiŵerenge Malemba ndi mabuku a nkhani za m’Baibulo ndiyeno nkumalingalira za zimene taŵerengazo nkuzigwiritsira ntchito. Kusunga maubwenzi abwino nthaŵi zonse kumafuna kuyesetsa. Nchiyaninso chingakhale chaphindu kwambiri kusiyana nkukulitsa chikondi chathu pa Yehova ndi Mwana wake? Chotero tiyeni tiyesetse kukhala ndi njala yabwino yauzimu kuti tisonyeze kuti ndife mabwenzi a Mulungu ndi Kristu.