Lingaliro
September ndi mwezi wachisanu ndi chiŵiri tikugaŵira buku la Chidziŵitso. Pamene kuli koti tikufunadi kusumika maganizo pa chothandiza kuphunzira Baibulo chabwino chimenechi, kumbukirani kuti mabuku ena a Sosaite amalongosola mwatsatanetsatane nkhani zochuluka zimene zalongosoledwa mwachidule m’buku la Chidziŵitso. Mungapititse patsogolo utumiki wanu mwa kuzoloŵerana ndi mabuku onse amene mpingo wanu uli nawo ndi kukhala watcheru kuti muzilimbikitsa ophunzira Baibulo ndi ena amene ali ndi chidwi pankhani inayake kuti awaŵerenge.