Onse Ayenera ‘Kulandira Mawu Mofunitsitsa’!
1 Anthu mamiliyoni ochuluka akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kuti ayenerere moyo wosatha, ayenera ‘kulandira mawu mofunitsitsa,’ monga momwe anachitira anthu 3,000 amene analapa ndi kubatizidwa patsiku la Pentekoste mu 33 C.E. (Mac. 2:41, NW) Kodi zimenezi zimatipatsa ntchito yotani lerolino?
2 Tiyenera kuthandiza ophunzira Baibulo athu kuwonjezera kukonda Yehova. (1 Tim. 4:7-10) Pa mbali imeneyi, mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, ndime 20, inapereka lingaliro lakuti: “Nthaŵi zonse pamene mukuphunzira, funafunani mipata yokulitsira chiyamikiro pa mikhalidwe ya Yehova. Nenani mawu osonyeza chiyamikiro cha inu mwini choona mtima kaamba ka Mulungu. Thandizani wophunzira kuganiza za kukulitsa unansi wake wachikondi ndi Yehova.”
3 Vuto Limene Timakumana Nalo: Anthu ambiri, pokhala atasonkhezeredwa ndi chipembedzo chonyenga, ndi okhutira ndi kalambiridwe kamene sikamafuna nthaŵi yochuluka ndi kuyesetsa, kosafuna kuti achite kusintha moyo wawo. (2 Tim. 3:5) Ntchito imene tili nayo njakuthandiza ophunzira Baibulo athu kuzindikira kuti kulambira koona kumafuna zambiri, osati kungokhala akumva mawu a Mulungu chabe. Zimene akuphunzira ayenera kuzigwiritsa ntchito pamoyo wawo. (Yak. 1:22-25) Ngati chinachake chokhudza khalidwe lawo nchosavomerezeka ndi Mulungu, afunikira kuzindikira kuti akuyenera ‘kubwerera’ ndi kuchita chimene chili choyenera kuti amsangalatse. (Mac. 3:19) Kuti akapeze moyo wosatha, ayenera ‘kuyesetsa’ ndi kugwiritsitsa choonadi.—Luka 13:24, 25.
4 Pokambitsirana nkhani zosiyanasiyana zokhudza makhalidwe abwino, mfunseni wophunzira Baibulo wanu mmene iyeyo amaonera nkhani zimenezi ndi zimene angachite ngati aona kuti akufunika kusintha moyo wake. Mchititseni kukhala ndi chidwi ndi gulu limene akuphunzira nalo choonadi, ndipo mulimbikitseni kuti azifika pamisonkhano ya mpingo mokhazikika.—Aheb. 10:25.
5 Tiyeni tichipange kukhala cholinga chathu kuti zimene tikumphunzitsa wophunzira wathuyo zizimfika pamtima. Tidzasangalala pamene tisonkhezera achatsopano kulandira mawu a Mulungu mofunitsitsa nabatizidwa!—1 Ates. 2:13.