Mitu ya Mabanja—Kodi Mukusamalira Udindo Wanu Wachikristu?
1 Ndi dalitso lalikulu chotani kukhala ndi ana amene amakonda kutumikira Yehova! Nchisangalalo chachikuludi chimene chimakhala m’mitima ya makolo okhulupirika. Mtumwi Yohane anasonyeza kuti anali kumva motero ponena za ana ake auzimu pamene analemba kuti, “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.”—3 Yoh. 4.
2 Ngati muli mutu wa banja, mungakhale ndi mlandu kwa Mulungu ngati banja lanu simukulidyetsa bwino mwauzimu. Monga momwe chakudya chakuthupi chopatsa thanzi chimawonjezera thanzi labwino, inuyo ndi banja lanu mumafunikira chakudya chauzimu chochuluka nthaŵi zonse kuti mukhalebe “olama m’chikhulupiriro.” (Tito 1:13) Ngati muli ndi ana m’nyumba mwanu, Mulungu adzakuyamikirani chifukwa chowapatsa malangizo auzimu abwino.
3 Makolo ambiri amafunsa kuti: “Kodi mumatani kuti ana anu azikhala auzimu?” Funsoli nlomveka pamene tiona zinthu zausatana zimene ana akukakamizidwa kuchita lerolino. Yankho la makolo amene achitapo bwino lili lothandiza: “Chofunika chachikulu ndicho chakuti iweyo uziwapatsa chitsanzo chabwino pa zinthu zauzimu.”
4 Udindo Wanu Makolo: Makolo achikristu, makamaka atate, ali ndi udindo wophunzitsa ana awo kukhala olambira a Yehova. Zimenezi sizitanthauza kumangochita nawo phunziro la Baibulo la banja, komanso kupita nawo mu utumiki wakumunda, kuwaphunzitsa kuti akhale ofalitsa uthenga wabwino. Ana angaphunzitsidwe kugaŵira mathirakiti, kuŵerenga malemba, kusonyeza magazini a Nsanja ya Olonda ndi kupereka ndemanga zachidule mogwirizana ndi msinkhu wawo. Safunika kutsala panyumba pamene makolo awo apita mu utumuki wakumunda. Ayenera kuphunzitsidwa njira imene ayenera kuyendamo. Ana amapita patsogolo kwambiri mwauzimu pamene achita utumiki wakumunda ndi makolo awo. M’zochitika zina, mkulu kapena mbale kaya mlongo wina wofikapo angapereke chithandizo, molingana ndi zimene zikufunika mu mkhalidwe uliwonse. Zoona, makonzedwe amenewo sayenera kutengedwa ngati chopeputsira ntchito ya m’Malemba ya makolo, makamaka ya atate, yophunzitsa, kulangiza ndi kusamalira ana awo.—Deut. 6:6, 7; 1 Tim. 3:2, 4. Onani buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 99, 100.
5 Kuti ana apite patsogolo kwambiri, amafunika kukhala ndi mabaibulo awoawo ndiponso mabuku amene timaphunzira pamisonkhano. Amafunika kuthandizidwa kukonzekera mayankho ndi kuyankha pamisonkhano. Alimbikitseni kulembetsa Sukulu Yautumiki Wateokrase ndipo athandizeni kuti azitanganidwa ndi zinthu zateokrase. Akulu angagwiritsire ntchito ana ena kuchitira chitsanzo ulaliki wosavuta. Aloŵetseni m’mapologalamu a Msonkhano wa Utumiki kuti azinena za zokumana nazo zawo za kusukulu ndi muutumiki wakumunda. Zimenezi zidzawonjezera chimwemwe cha mpingo wonse komanso cha achinyamatawo. Musanyalanyaze kugwiritsa ntchito achinyamata ndi ana. Yesu anati: “Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.”—Mat. 19:14.
6 Aphunzitseni Kuti Kufika Pamisonkhano Nkofunika: Mwana amafunika chilangizo cha Baibulo ngati ati adzakhale ndi moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Kuti mwana aphunzire kukonda zinthu zauzimu afunikira kumafika pamisonkhano. Panthaŵi zina, makolo amakayikira kupita ndi ana awo kumisonkhano chifukwa choopa kuti azikasokoneza anthu ena. Ena amasiya ana awo kunyumba kuti azigwira ntchito yawo ya kusukulu. Komabe kholo lanzeru limapita ndi ana ake kumisonkhano.—Deut. 31:12.
7 Chinthu choyambirira chimene mwana ayenera kuphunzira kuchokera paukhanda ndi chakuti amapita ku Nyumba ya Ufumu kukamvetsera. Koma ngati amapatsidwa zinthu zoti zizimtanganitsa, monga ngati zidole kapena chakudya, kapenanso ngati amaloledwa kumaseŵera pamalo amene wakhala, kodi adzaphunzira kumvetsera ndi kuzindikira chifukwa chake timafika pamisonkhano pa Nyumba ya Ufumu? Nzoona kuti ana ena amamvetsera kwambiri kusiyana ndi ena. Komabe, pamene mwana wachita zosokoneza, kholo lanzeru limamuongolera ndipo mwachikondi nkumphunzitsa kuti azimvetsera, osati mwa kumunyengerera ndi masuwiti kapena zidole, koma mwa kugwiritsa ntchito chilangizo cha Mawu a Mulungu.—Miy. 13:24; Aef. 6:4.
8 Anthu a Mulungu ali ngati banja lalikulu. Tonse timasangalala kukhala ndi ena, kuphatikizapo ana. Atafika pamisonkhano yampingo pa Nyumba ya Ufumu, mwamuna ndi mkazi, limodzi ndi ana awo, ayenera kukhala pamodzi osati kusiyanitsidwa. Makolo angayamikire ngati athandizidwa kusamalira ana awo pamisonkhano ndiponso kuwathandiza muutumiki wakumunda. Ana azidziŵa kuti timawasoŵa ngati sanafike ku Nyumba ya Ufumu. Auzeni mmene achatsopano omwe amafika pa Nyumba ya Ufumu amayamikirira chitsanzo chawo chabwino.
9 Pamene mukuunguzaunguza anthu pa Nyumba ya Ufumu, yang’anitsitsani abale ndi alongo achichepere amene amawonjezera mzimu wabwino wampingo. Kodi sitili oyamikira kuti akumbukira Mlengi wawo Wamkulu m’masiku a unyamata wawo? (Mlal. 12:1) Ndithudi anyamata ndi atsikana ameneŵa amapereka chitsanzo chabwino chifukwa makolo awo anayesetsa kuwaphunzitsa bwino kwambiri, ndipo tingofunikira kufunsa makolo awowo kuti atitsimikizire zimenezi. Komabe, kodi nchiyani chimene chimafunikira pa kuphunzitsa mwana njira yoyenera?—Miy. 22:6.
10 Mkristu aliyense amene wakhalapo ndi banja angavomereze mwamsanga kuti imeneyi si ntchito yapafupi. Komabe, Mawu ouziridwa a Mulungu amasonyeza makolo zinthu zingapo zofunika. Chimodzi ndicho kuyamba pamene anawo ali aang’ono. Ali aang’ono motani? Pamene Aisrayeli anali kusonkhana kuti alandire malangizo kuchokera kwa Yehova, “makanda” anali kukhalaponso. (Deut. 29:10-13; 31:12, 13) Mwachionekere, akazi achiisrayeli anali kubwera ndi ana awo akhanda panthaŵi zimenezi, popeza kuti onse anali kufunika kuti akapezekepo. Kungoyambira ‘paukhanda,’ ana awo aamuna ndi aakazi anali kuphunzira kufunika kokhala chete ndi kumvetsera pamisonkhano. (2 Tim. 3:15) Motero pitani ku misonkhano ndi “makanda” anu. Ndiponso, aloŵetseni mu utumiki wakumunda mwamsanga pamene ali okhoza kutero. Laŵirirani kuyamba kuphunzitsa “makanda” anu “kuopa Yehova,” mwapang’onopang’ono.
11 Motero mwa kuyambira ‘paukhanda’ kuphunzitsa ana anu, kuchita nawo phunziro la Baibulo la banja mokhazikika, kupita nawo ku misonkhano yampingo mokhulupirika, ndi kuwaphunzitsa utumiki wakumunda, mitu ya mabanja idzakhala ikusamalira udindo wawo wachikristu. Ndithudi tidzakhala ndi madalitso a Yehova.—Miy. 10:22.