Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/99 tsamba 1
  • Chikumbutso cha Imfa ya Kristu Chapadziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikumbutso cha Imfa ya Kristu Chapadziko Lonse
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Muziyamikira Zimene Yehova Ndi Yesu Anakuchitirani
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mwambo wa Chikumbutso Umasonyeza Makhalidwe a Mfumu Yakumwamba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu
    Nsanja ya Olonda—2003
  • N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 3/99 tsamba 1

Chikumbutso cha Imfa ya Kristu Chapadziko Lonse

1 Yehova watipatsa mphatso zambiri zedi. Ubwino wake ndi kukoma mtima kwake konse zafotokozedwa bwino lomwe monga ‘mphatso yosatheka kuneneka.’ Inde, “chisomo choposa cha Mulungu” n’chodabwitsa kwambiri chosatheka kwa ife kuchifotokoza.—2 Akor. 9:14, 15.

2 Mphatso Yake Yaikulu Koposa Zonse: Yesu Kristu, monga Mombolo wa mtundu wa anthu, ndi mphatso yaikulu koposa zonse. Posonyeza chikondi chake chachikulu pa dziko la anthu, Yehova anapereka Mwana wake wokondedwa komanso wobadwa yekha. (Yoh. 3:16) Dalitso lachisomo lochokera kwa Mulungu limeneli n’lofunikadi kulikumbukira padziko lonse. Liti ndipo motani? Lachinayi pa April 1, 1999, madzulo, Akristu padziko lonse adzakumbukira Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, mwakuchita Chikumbutso cha nsembe yaikulu koposa zonse.—1 Akor. 11:20, 23-26.

3 Kristu adatifera “pokhala ife chikhalire ochimwa,” ndipo aliyense wa ife angasonyeze chiyamikiro chake mwa kupezeka pa Chikumbutso cha imfa yake ndiponso mwa kuitana ena kuti adzakhale nawo pachochitika chofunika kwambiri chimenechi.—Aroma 5:8.

4 Chochitika Chofunika Kwambiri: Kukumbukira imfa ya Kristu kwenikweni kumasonyeza kuti anachirikiza mosalakwa uchifumu wa Mulungu. Chimatikumbutsanso kuti tingakhale ndi kaimidwe kabwino ndi Yehova mwa kusonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu, kenako kupeza chipulumutso. (Mac. 4:12) Ndithudi, chimenechi n’chochitika chofunika kwambiri pachaka!

5 Timasonyeza kukonda anansi athu mwa kuwaitana kudzakhala nafe pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Mapindu a dipo akugwirabe ntchito kwa mamiliyoni a anthu omwe akuphunzira za kupambana kwake. (Afil. 3:8) Amene akusonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya Kristu angapeze chiyembekezo cholimba cha moyo wosatha.—Yoh. 17:3.

6 Nyengo ya Chikumbutso imatipatsa mpata wapadera wosonyezera kuyamikira kwathu chisomo choposa cha Mulungu. Imeneyi ndi nthaŵi yabwino kwambiri yolalikira mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Mapindu ochuluka akudikira onse amene amasonyeza kuyamikira mphatso yaulere yosaneneka ya Yehova ndiponso akukonzekera kudzapezeka paphwando la chaka chino la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena