Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu August: Lililonse la mabolosha a masamba 32 ali m’munsiŵa angagwiritsidwe ntchito: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabolosha a Buku la Anthu Onse, ndi Mizimu ya Akufa—Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? angagaŵiridwe pamene kuli koyenera. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati paulendo wobwereza mwapeza okondwerera, mungagaŵire masabusikiripishoni. November: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
◼ Pachaka m’dziko lililonse nthaŵi zina pamakhala maholide amene ana asukulu ndi anthu ogwira ntchito amapatsidwa tchuthi. Imeneyi ndi nthaŵi yabwino kwambiri yakuti mpingo ukhale ndi nthaŵi yochuluka yochita utumiki wakumunda. Akulu ayenera kukonzekereratu nthaŵi zimenezi ndi kudziŵitsiratu mpingo za makonzedwe amene akupangidwa ochita umboni wa kagulu masiku a holide.
◼ Mafomu okwanira oti agwiritsidwe ntchito m’chaka chautumiki cha 2000 akutumizidwa ku mpingo uliwonse. Chonde gwiritsani ntchito mafomuŵa moyenera. Ayenera kugwiritsidwa ntchito kokha pantchito imene anapangidwira.
◼ Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-18). Mlembi wa mpingo ayenera kukumana ndi mtumiki wa mabuku kumayambiriro kwa August ndi kupangana tsiku loti adzaŵerengere mabuku amene mpingo uli nawo pamapeto pa mweziwo. Mabuku onse amene ali m’sitoko ayenera kuŵerengedwa, ndipo ziwonkhetso zake zilembedwe pafomu ya Kuŵerengera Mabuku. Chiŵerengero cha magazini amene alipo mungachipeze kwa mtumiki wa magazini. Chonde tumizani pepala loyamba ku Sosaite pasanafike pa September 6. Sungani pepala lachiŵiri m’fayelo yanu. Pepala lachitatulo mungaligwiritse ntchito ngati poŵerengerera. Kuŵerengeraku kuyenera kuyang’aniridwa ndi mlembi, ndipo fomu yodzazidwayo ipendedwe ndi woyang’anira wotsogoza. Mlembi ndi woyang’anira wotsogoza asaine fomuyo.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kalendala ya Mboni za Yehova ya 2000 pa fomu yawo yoodera mabuku ya September. Makalendala adzakhalako mu Chicheŵa ndi Chingelezi.