Lipoti la Mmene Ntchito Yomanga Nthambi ya Malaŵi Ikuyendera
1 Zaka mazana ambiri zapitazo, wamasalmo wouziridwa analemba izi pa Salmo 127:1: “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.” Ndi mmene ntchito ikuyendera pamalo a nthambi yatsopano ku Lilongwe, zili zosakayikitsa kuti amene akuimanga akugwira ntchito zolimba. Zilinso zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa ntchitoyi chifukwatu atumiki a Mulungu ambirimbiri apereka ndalama zawo, mphamvu, nthaŵi, ndi maluso awo kuti amange nthambiyi imene idzachirikiza zinthu za Ufumu wopambana wa Yehova m’dziko lonse la Malaŵi.
2 Anthu ambiri amene akuona mmene ntchitoyi ikugwiridwira mofulumira anena kuti: ‘Ndithudi Yehova akufuna kuti ntchitoyi ithe mwamsanga.’ Ena ananena kuti, “Izi n’zodabwitsa. Mulungu ayeneradi kuti ali nanu!” Ameneŵa ndiwo mawu amene amamveka kaŵirikaŵiri m’makampani amene amatigulitsa zipangizo zogwiritsa ntchito pamalo achimangoŵa. Inde, izidi “n’zodabwitsa,” chifukwa ndi anthu a Yehova okha amene, kupyolera mwa mzimu wa Yehova, angathe kuchita zinthu zooneka ngati zosatheka. Zili monga mmene Yehova ananenera kwa Mfumu Zerubabele pa Zekariya 4:6 kuti: “Ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.”
3 Inde, malingaliro amenewo akusonyeza chidaliro chakuti mzimu wofunitsitsa ndi kugwira ntchito zolimba kwa anthu ake zili zofunika kwambiri, limodzinso ndi madalitso ochuluka a Mulungu. Zikufanana ndi zimene Paulo ananena pa 1 Akorinto 3:7 kuti, ‘Mulungu amakulitsa.’ Ndithudi kudziŵa kuti Yehova akuchirikiza ntchitoyi kumalimbikitsa onse amene ali ndi mwayi wogwira nawo ntchitoyi, popeza kuti amaona kuti ili mbali ya utumiki wawo wopatulika kwa iye. Tikukuthokozani nonse chifukwa cha kuchirikiza kwanu ntchitoyi kwa chaka chimodzi ndi theka zapitazi, ndipo tikukhulupirira kuti lipoti lino la mmene ntchitoyi ikuyendera lidzakulimbikitsani kupitiriza kuichirikiza mpaka ntchito yonse itatha.
4 Kudzipereka Eni Ake: Atumiki apadziko lonse m’ntchito za chimango okwanira 29 ochokera m’mayiko 22 anatumizidwa kudzagwira ntchitoyi. Abale akunja ameneŵa akugwira ntchito limodzi ndi abale ndi alongo 41 a kuno ku Malaŵi a banja la Beteli koma omwe akugwira ntchito ku chimango. Ndiponso, antchito odzifunira apadziko lonse oposa 90 athandizapo pa ntchitoyi kwa masabata oyambira pa aŵiri kufika pa miyezi itatu kapena kuposerapo. Abale ndi alongo ameneŵa analipira okha ulendo wobwera kudzagwira ntchito kuno ndiponso aphunzitsa abale a kuno maluso osiyanasiyana a zomangamanga popeza kuti abale ambiri a kuno sali ozoloŵera kwambiri ntchito ya zomangamanga. Iwo aphunzira kugwiritsa ntchito makina osiyanasiyana ogwiritsidwa ntchito pazomangamanga, kusakaniza ndi kukonza bwinobwino konkire, kupaka penti, kupanga pulasitala ndiponso kulumikiza zitsulo zogwiritsa ntchito pomanga. Awo amene anazoloŵera kugwira ntchitozi ali ndi chikhumbo chophunzitsa ena zimene akudziŵazo, chifukwa palibe amene amaopa kuti wina amulanda ntchito popeza kuti pali ntchito yokwanira aliyense. Aliyense ndi wosonkhezereka mwamphamvu kuti ntchito yake aigwire bwino kusonyeza chikondi chake kwa Mulungu. Pa mapeto a mlungu, anthu odzipereka ochokera m’mipingo yapafupi amabwera kudzagwira nawo ntchitoyi. Zonsezi zimasonyeza kuti anthu akuthandiza kwambiri ntchitoyi ndipo tikuyamikira ndi mtima wonse.
5 Kuphatikiza pa kumanga nyumba zenizenizo, chimango cha mtundu winanso chakhala chikuchitika. Ichi ndi kumangidwa kwa ubale wa padziko lonse, ndipo pakhaladi kulimbikitsana kwambiri. Pang’ono chabe tikuona ‘khamu lalikulu lochokera mu mtundu uliwonse’ likugwira ntchito limodzi mogwirizana kuti likwaniritse chifuno cha Yehova.—Chiv. 7:9.
6 “Ndi Chuma Chako”: Zoonadi, sikuti aliyense angabwere kudzagwira nawo ntchitoyi chifukwa cha kukhala kutali, matenda, kapena mikhalidwe ina. Komabe tonsefe tingathe kugwira nawo ntchito imeneyi mwa njira ina yake, mosasamala kanthu za kumene timakhala, ndipo njirayi ndi mwa zopereka zathu zaufulu. Miyambo 3:9 imati: “Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha.”
7 Mtumwi Paulo anapereka malingaliro abwino pa 1 Akorinto 16:2 pamene anati: “Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula.” Mwa kutsatira zimenezi, mipingo yambiri ikutumiza zopereka mowoloŵa manja ku thumba la chimango pamodzi ndi ndalama zomwe imatumiza mwezi ndi mwezi. Ngati inunso mukufuna kulemekeza Yehova ndi chuma chanu, muzilemba pa zopereka zanuzo kuti “Zopereka za Chimango cha Nthambi” kuti muzisiyanitse ndi zopereka zina zonse.
8 Mwina mukudziŵa kuti maofesi a nthambi yatsopano ali m’mphepete mwa Msewu wa Chilambula ku Area 32 ku Lilongwe. Pofika mapeto a October, kupitirira theka la ntchitoyi inali itatha. Mungasangalale kumva kuti ziŵiri mwa nyumba zitatu zogonamo tsopano munalowa anthu, nyumba iliyonse ndi yokwana anthu 40. Maziko a Nyumba Yogona Yachitatu akuyalidwa ndipo ntchitoyo ikuyenda bwino.
9 Kumbali ina pamalo a chimangowo, ntchito yokonza Nyumba yosanjikizana ya Maofesi ndi Mautumiki Osamalira Antchito a pa Beteli ikuyenda bwino. Zipinda zapansi za nyumbayi padzakhala khomo loloŵerapo anthu onse komanso malo olandirira alendo, mudzakhalanso khichini, chipinda chodyera, kochapira zovala ndi Ofesi ya Beteli. Pamwamba padzakhala Dipatimenti Yoyang’anira Utumiki, imene ikusamalira mipingo yoposa 635. Pamwambapo padzakhalanso Dipatimenti Yotembenuza, imene tsopano ikutembenuzira mabuku mu Chicheŵa ndi Chitumbuka. Posachedwapa idzayamba kutembenuzira mu Chiyao. Madipatimenti ena monga ngati Dipatimenti Yopereka Chidziŵitso cha Zachipatala ndi Dipatimenti Yomanga Nyumba za Ufumu adzakhalanso pa nsanjika imeneyi. Tikukhulupirira kuti pofika pa January 1, 2000, nyumba imeneyi idzakhala ikugwiritsidwa ntchito. Nyumba ina ya maofesi yosanjikizana yocheperapo, imene yagundikizana ndi Nyumba ya Maofesi ndi Mautumiki Osamalira Antchito a pa Beteli chakummaŵa kwake, idzamalizidwa pofika mu June 2000.
10 M’Nyumba Yosungiramo Katundu imene ili pafupi ndi Nyumba ya Maofesi ndi Mautumiki Osamalira Antchito a pa Beteli chakumadzulo kwake, mudzakhala Dipatimenti Yotumiza Mabuku, chipinda chotengerako mabuku a Mpingo, ndi Dipatimenti Yogula Zinthu komanso Dipatimenti Yokonza Zinthu Zowonongeka. Nyumba ya Ufumu ndi Galaja zimene zili tsidya lina la msewu kuchokera pamene pali Nyumba ya Maofesi ndi Mautumiki Osamalira Antchito a pa Beteli nazonso zatsala pang’ono kutha.
11 Kodi chimango chonse chidzatha liti? Ndi mmene tikuchirikizidwira, ntchitoyi iyenera kumalizidwa pofika mwina mu July 2000. Tikukhulupirira kuti ambiri a inu mudzathandizapo, osati kokha amene ali m’mipingo yozungulira. Uli mwayi umene ungabwere kamodzi kokha. Musauphonye! Monga tinanena poyambapo, kwa nthaŵi yaitali ndithu tsopano abale akhala akubwera kudzagwira ntchito pa mapeto a mlungu umene anauzidwa. Tikuyamikira kwambiri thandizo la onse amene akhala akubwera kudzagwira ntchitoyi.
12 Kumanga maofesi a nthambi yatsopano ndi chinthu chosaiŵalika kwa Mboni za Yehova m’Malaŵi, ndipo chikutikumbutsa nthaŵi zachisangalalo za m’mbuyomo. Timakumbukira kusangalala kwa Aisrayeli pamene anali kumanga chihema. Kuyala maziko a kachisi mu Yerusalemu m’masiku a Ezara kunalinso chochitika china chosangalatsa kwambiri. Ponena za nthaŵi imeneyo Baibulo limati: “Anthu sanazindikira phokoso la kufuula mokondwera kulisiyanitsa ndi phokoso la kulira kwa anthu; pakuti anthu anafuulitsa kwakukulu, ndi phokoso lake lidamveka kutali.”—Ezara 3:13.
13 Ndi zokondweretsa kuona kuti ntchito ikufutukuka m’Malaŵi. Kumanga maofesi a nthambi yatsopano kwapereka mwayi wabwino zedi wopereka umboni wabwino kwambiri ndipo kwalimbikitsa chikhulupiriro cha onse amene agwira nawo ntchitoyo. Tikukuthokozani ndi kukuyamikani chifukwa cha kuchirikiza chimangochi mwaufulu kufika lerolino. Tonse tipitirizetu kuchirikiza ntchitoyi mwa kupempha madalitso a Yehova, ndiponso mwa kupitiriza kupereka ndi mtima wonse nthaŵi yathu ndi chuma chathu, kuti iye atamandike ndi kuti apatsidwe ulemerero.—Aroma 15:11.
[Zithunzi patsamba 4]
1. Kuika malata pa Nyumba ya Ufumu
2. Abale a m’mayiko osiyanasiyana akugwira ntchito pamodzi kuika zitsulo zogwira denga
4. Kuphunzitsidwa ntchito ndi abale a kumayiko ena
5. Abale achimalaŵi ophunzitsidwa ntchito ya magetsi
6. Antchito ya m’khichini akuphika chakudya cha antchito 100 anjala
[Zithunzi patsamba 5]
3. Limodzi mwa makoma akonkire opitirira 460 likuikidwa m’malo ake
7. Nyumba yosanja ya Maofesi ndi ya Mautumiki Osamalira Antchito komanso nyumba zogonamo yoyamba ndi yachichiwiri kumbuyo kwake
8, 9. Abale achimalaŵi ophunzitsidwa akusanganiza ndi kumaliza ina ya konkire yoposa makyubiki mita 2,000
[Chithunzi patsamba 6]
Banja la Beteli ndi atumiki apadziko lonse ndi antchito yodzifunira apadziko lonse