Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/99 tsamba 7
  • Tetezani Nyumba za Ufumu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tetezani Nyumba za Ufumu!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 11/99 tsamba 7

Tetezani Nyumba za Ufumu!

1 Chifukwa cha kuipa kwa masiku ano tifunika kulingalira bwino pa kuteteza Nyumba ya Ufumu. Choncho, funso n’lakuti, Kodi tingateteze bwanji Nyumba za Ufumu? Monga mmene timatsatirira malangizo kuti nyumba zathu zikhale zosungika ndi zotetezeka, tiyeneranso kutero ndi Nyumba zathu za Ufumu. Ndi udindo wa akulu kuona kuti Nyumba ya Ufumu iliyonse ili ndi chitetezo chokwanira. Palidi kufunika kochita zimenezi chifukwa tikumva malipoti ambiri m’madera osiyanasiyana a anthu owononga zinthu ndi akuba.

2 Chofunika pa chitetezo chabwino chingakhale kutseka ndi kukhoma bwinobwino zitseko zonse, mageti ndi mawindo nthaŵi zonse pamene mwagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu. Abale okhoza kuchita zinthu ndi odalirika ayenera kuyang’anira makonzedwe a ntchito ya chitetezo imeneyi nthaŵi iliyonse pamene Nyumba ya Ufumu ikugwiritsidwa ntchito. Izi zikuphatikizapo nthaŵi imene Nyumba ya Ufumu yagwiritsidwa ntchito pa zochitika zina, monga ukwati kapena kuyeretsa, osati pamisonkhano yampingo ya nthaŵi zonse yokha.

3 Ngati Nyumba ya Ufumu ili ndi malo oimikapo galimoto, kuli bwino kuti pazikhala powala bwino panthaŵi imene kuli mdima. Izi zidzachepetsa anthu kuwononga galimoto kapena njinga komanso kupweteka kapena kuvulaza abale ndi alongo pochoka m’Nyumba ya Ufumu. Mipingo ina yaona kuti n’koyenera kukhala ndi akalinde n’kumasinthana kukhala panja pa Nyumba ya Ufumu misonkhano ili mkati kupeŵa mbala ndi anthu owononga zinthu.

4 Mipingo ina imaona kukhala koyenera kukhoma zitseko misonkhano ili m’kati. Kumalo oipitsitsa kumene izi zingakhale zofunika, akalinde odalirika ayenera kuima pakhomo nthaŵi zonse kuti aziona amene akuloŵa m’Nyumba ya Ufumu. Bungwe la akulu liyenera kusankha zoyenera kuchita mogwirizana ndi malamulo a kumaloko okhudza malo osonkhanira. Ngati makonzedwe ameneŵa aikidwa, mpingo uyenera kudziŵitsidwa zimenezi kuti uzidziŵiratu kuti khomo la Nyumba ya Ufumu lizikhala lokhoma.

5 Tikufuna kuti abale ndi achatsopano azikhala motetezeka pofika pamisonkhano pa Nyumba ya Ufumu ndipo tikufuna kuteteza malowo kwa anthu owononga zinthu ndi akuba. Choncho akulu mu mpingo uliwonse ayenera kupenda mikhalidwe yofala kumaloko kenako n’kuchita mogwirizana ndi zimenezo kuti ateteze Nyumba ya Ufumu ndi opezeka pamisonkhano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena