Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/00 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 5/00 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Khalani ndi bulosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu achidwi, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Ikani maganizo pa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha a masamba 32 ali m’munsiŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhalako Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, Mabulosha a Buku la Anthu Onse, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? angagaŵiridwe pamene kuli koyenera kutero.

◼ Woyang’anira wotsogolera ayenera kudziŵitsa Sosaite ku Lilongwe ngati mwezi umenewo sakulandira Utumiki Wathu wa Ufumu ndi magazini za mwezi wotsatira.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa June 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detilo. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mutatha kupereka lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Potithandiza kuti tikonzekere ndi kuimba nawo mokwanira pa Misonkhano Yachigawo ya chaka chino yakuti “Akuchita Mawu a Mulungu,” Sosaite yasankha kukagwiritsira ntchito nyimbo zotsatirazi: 19, 42, 85, 91, 107, 111, 112, 113, 123, 155, 160, 164, 175, 177, 181, 191, 201, 202. Tiyenitu tonse tiziyesereretu nyimbozi kuti tikaimbire Yehova zitamando mwamphamvu ndiponso mwachimwemwe.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:

◼ Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba—Chicheŵa

◼ Yehova—Kodi Iye Ndani? (Thirakiti Na. 23)—Chicheŵa, Chitumbuka

◼ Yesu—Kodi Iye Ndani? (Thirakiti Na. 24)—Chicheŵa, Chitumbuka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena