Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Makope amagazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Paulendo wobwereza mukapeza okondwerera, mungagaŵire masabusikiripishoni. Kuyambira kumapeto kwa mwezi uno, tidzagaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. November: Tidzapitiriza kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Mipingo imene idzamalize kugaŵira eninyumba onse Uthenga wa Ufumu Na. 36 m’gawo lawo ingagaŵire bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso. December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.
◼ Nambala ya telefoni ya ofesi ya nthambi ya Sosaite ku Lilongwe, yasinthidwa. Nambala yakale imene inali 782392 sikugwiritsidwanso ntchito. Nambala yatsopano ndi 762111.
◼ Akulu akukumbutsidwa kutsatira malangizo operekedwa pamasamba 21-3 a Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, onena za wochotsedwa aliyense kapena munthu wodzilekanitsa amene angakonde kubwezeretsedwa.
◼ Amene akugwirizana ndi mpingo ayenera kutumiza masabusikiripishoni onse atsopano komanso olembetsanso a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kuphatikizapo masabusikiripishoni awoawo, kupyolera mumpingo.
◼ Sosaite silembera wofalitsa oda ya mabuku amene akufuna. Woyang’anira wotsogolera azikonza chilengezo mwezi uliwonse asanatumize oda yamabuku ya mwezi ndi mwezi yampingo ku sosaite kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale wosamalira mabuku. Chonde kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera.
◼ Kuyambira pa September 1, 2000, padzakhala kusintha kwakukulu pafupifupi m’madera onse m’Malaŵi muno. Mpaka pa August 31, 2000, takhala tili ndi madera 24 ogaŵidwa m’zigawo zitatu. Kuyambira pa September 1, 2000, mudzakhala madera achicheŵa 33 ndi dera limodzi lachingelezi. Mpingo uliwonse wauzidwa dera lake latsopano ndiponso woyang’adera dera wawo watsopano. Popeza malo a mpingo uliwonse sanasinthe, malo akale otulako mabuku apitirira kugwiritsidwa ntchito. Dera lililonse liziyamba ndi mipingo yosaposa 25 ndiponso yosachepera pa mipingo 18. Iyi ndi nkhani yabwino chifukwa zikutanthauza kuti woyang’anira dera azitha kukonza ulendo wochezera mpingo uliwonse m’miyezi isanu ndi umodzi. Tikuthokoza Yehova chifukwa cha zimenezi.
◼ Kuyambira ndi kope la September 1, 2000, Nsanja ya Olonda idzayamba kutuluka m’Chitumbuka kamodzi pamwezi.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo pambuyo pa lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kalendala ya Mboni za Yehova ya 2001 pa fomu yawo yofunsira mabuku ya September. Makalendala adzakhalako m’Chicheŵa, Chingelezi ndi m’Chitumbuka. Zimenezi n’zaoda yapadera.
◼ Tikupempha onse amene amapita kunthambi kukasiya ma S-20 kuchokera m’mipingo yosiyanasiyana kuti chonde azipita Lachiŵiri kapena Lachinayi. Tidzayamikira kwambiri kusamalira kwanu nkhaniyi.
(Zapitirizidwa pa tsa. 4, danga 1)
Zilengezo(Zapitirizidwa)