Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase
Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa
September 4 kufikira December 18, 2000. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Davide analetsa Abisai kupha Simeyi chifukwa chakuti Davide anali wolakwa pa zimene Simeyi ankam’nenera. (2 Sam. 16:5-13) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 5/1 tsa. 32 ndime 3.]
2. Chikumbumtima choyera, chophunzitsidwa bwino sichingotithandiza kuti tikhale paunansi wolimba ndi Mulungu kokha basi koma n’chothandizanso kwambiri pa chipulumutso chathu. (Aheb. 10:22; 1 Pet. 1:15, 16) [w98-CN 9/1 tsa. 4 ndime 4]
3. Cholinga chodziŵira mawu ochuluka ndicho kudzionetsera kwa anthu akudziko kuti Mboni za Yehova zimadziŵa bwino zinthu ndiponso n’zaluso. [sg-CN tsa. 55 ndime 7]
4. Ulamuliro wa zaka 1,000 wa Yesu ungafanizidwe ndi ulamuliro wa zaka 40 wamtendere ndi wachitukuko wa Solomo. (1 Maf. 4:24, 25, 29) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 6/1 tsa. 6 ndime 5.]
5. Kuikidwa m’manda mwaulemu kwa Abiya kunali umboni woonekeratu wakuti iye anali wolambira wokhulupirika wa Yehova, anali wolambira yekhayo wokhulupirika wa m’nyumba ya Yerobiamu. (1 Maf. 14:10, 13) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 4/1 tsa. 12 ndime 11.]
6. Kubatizidwa mwachikristu kumasonyeza kuti munthu wobatizidwayo wakhala mtumiki wokhwima m’nzeru wa Mulungu. [w98-CN 10/1 tsa. 28 ndime 2]
7. Yehova anapatsa mphamvu Eliya mwa kum’limbitsa mtima koposa kulimba mtima kwa munthu wathupi lanyama ndi kum’tchinjiriza ku mantha. (1 Maf. 18:17, 18, 21, 40, 46) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 1/1 tsa. 31 ndime 2.]
8. Zopakapaka m’maso pofuna kudzikongoletsa zinali zosadziŵika m’nthaŵi za Baibulo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani g77-E 9/22 tsa. 20.]
9. Khungu limene linagwa pa magulu ankhondo a Asuri chifukwa cha mawu a Elisa mwachionekere linali khungu la m’maganizo chifukwa chakuti iwo ankatha kumuona Elisa koma samatha kum’zindikira kuti ndani. (2 Maf. 6:18, 19) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani si mas. 70-1 ndime 10.]
10. Kuika “buku laumboni,” kotchulidwa pa 2 Mafumu 11:12, kunali kuchitira fanizo kophiphiritsira kuti matanthauzidwe a mfumu a Chilamulo cha Mulungu sanayenera kusinthidwa ndipo anayenera kumveredwa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 2/1 tsa. 31 ndime 6.]
Yankhani mafunso otsatiraŵa:
11. Mogwirizana ndi 1 Yohane 2:15-17, kodi makolo aumulungu ayenera kulimbikitsa ana awo kupewa chiyani pamene akuwathandiza kusankha ntchito yabwino? [w98-CN 7/15 tsa. 5 ndime 2]
12. Kodi n’chiyani chimene chimatanthauzidwa pa 2 Samueli 18:8, pamene pamati: “Nkhalango inawononga anthu akuposa amene anawonongeka ndi lupanga”? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87 3/15 tsa. 31 ndime 2.]
13. Kodi ndani amene lerolino angayerekezedwe ndi mabwenzi a Goliati, Arafa, ndipo n’chiyani chimene iwo amayesayesa kuchita? (2 Sam. 21:15-22) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 1/1 tsa. 20 ndime 8.]
14. Kodi mapindu aŵiri a kuyankhula kochokera m’maganizo ndi ati? [sg-CN mas. 59-60 ndime 5-7]
15. Kodi ndi mfundo yachikhalidwe yofunika iti imene tingaphunzire kuchokera pa zimene zinachitikira mwamuna wina amene anaphedwa chifukwa cha kuswa Sabata? (Num. 15:35) [w98-CN 9/1 tsa. 20 ndime 2]
16. Kodi ndi mwa kuchitanji mmene tingatsanzirire mfumu yaikazi ya ku Seba, imene inayenda ulendo wautali kukamva ‘nzeru za Solomo’? (1 Maf. 10:1-9) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 7/1 tsa. 31 ndime 1-2.]
17. Malinga ndi 1 Mafumu 17:3, 4, 7-9, 17-24, kodi ndi m’njira zitatu ziti zimene Eliya anasonyezera kukhulupirira Yehova? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 4/1 tsa. 19 ndime 5.]
18. Kodi n’chifukwa chiyani kukana kwa Naboti kupereka munda wake wa mpesa kwa Ahabu sikunali kusonyeza liuma? (1 Maf. 21:2, 3) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 8/1 tsa. 13 ndime 18.]
19. Kodi mawu a pa 2 Mafumu 6:16 alimbikitsa motani atumiki a Yehova lerolino? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 6/15 tsa. 18 ndime 5.]
20. Kodi ndi m’njira ziti zimene Akristu oona lerolino angapewere chisimoni? [w98-CN 11/15 tsa. 28 ndime 5]
Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Mkristu woona sayenera ․․․․․․․ ndi kuchita nawo miyambo imene sikondweretsa ․․․․․․․ . (Miy. 29:25; Mat. 10:28) [w98-CN 7/15 tsa. 20 ndime 5]
22. Polalikira kwa Mfumu Agripa, Paulo anali kuyankhula ․․․․․․․ , akumagogomezera nkhani zimene iye ndi Agripa anali ․․․․․․․ . (Mac. 26:2, 3, 26, 27) [w98-CN 9/1 tsa. 31 ndime 3]
23. Chifukwa chakuti Mulungu ․․․․․․․ , ena angalingalire kuti si weniweni, koma ․․․․․․․ mwakuya nthaŵi zonse kungathandize munthu “kuona wosaonekayo.” (Aheb. 11:27) [w98-CN 9/15 tsa. 21 ndime 3-4]
24. Monga momwe timaonera m’nkhani ya zimene zinachitikira ․․․․․․․ , kazembe wa ku Suriya, nthaŵi zina ․․․․․․․ pang’ono kumadzetsa mapindu aakulu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w99-CN 2/1 tsa. 3 ndime 6-tsa. 4 ndime 1.]
25. Monga momwe mtima wa Yehonadabu unalili ndi Mfumu Yehu, ․․․․․․․ lerolino limazindikira ndiponso kugwirizana ndi mtima wonse ndi Yehu Wamkulu, ․․․․․․․ , amene akuimiridwa padziko lapansi pano ndi ․․․․․․․ . (2 Maf. 10:15, 16) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 1/1 tsa. 13 ndime 5-6.]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Anali ( Satana; Yehova; Yoabu) amene anasonkhezera Davide kuchimwa mwa ‘kuŵerenga Israyeli.’ (2 Sam. 24:1) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 7/15 tsa. 5 ndime 2.]
27. Mogwirizana ndi 1 Mafumu 8:1 ndi Mlaliki 1:1, Solomo anasonkhanitsa anthu kuti (amange kachisi; athamangitse adani a Israyeli; alambire Yehova). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani si tsa. 112 ndime 3.]
28. Nyengo ya zaka 20 zimene Solomo anamanga kachisi ndi nyumba yake mu Yerusalemu imayerekezedwa ndi nyengo ya kuwongolera ziphunzitso ndi kulinganizidwa kwa gulu kumene kunayamba mu ( 1919; 1923; 1931) ndipo kumene kunatha mu ( 1938; 1942; 1950). (1 Maf. 9:10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 3/1 tsa. 20 bokosi.]
29. Mawu akuti “kumwamba” ogwiritsidwa ntchito pa 2 Mafumu 2:11 amanena za (malo auzimu kumene Mulungu amakhala; thambo lenileni; mlengalenga wa dziko, mmene mbalame zimauluka ndi mmene mphepo imaomba). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 9/15 tsa. 15 bokosi.]
30. Anali (Herode Wamkulu; Kaisara Augusto; Tiberiyo Kaisara) amene analamula kuti anthu aŵerengedwe zimene zinachititsa kuti Yesu abadwire ku Betelehemu m’malo mobadwira ku Nazarete. [w98-CN 12/15 tsa. 7 bokosi]
Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Sal. 15:4; Aef. 5:3, 4; 2 Maf. 1:2, 7, 8; 2 Maf. 3:11; Akol. 3:13
31. Mawu a Mulungu amatithandiza kuona nkhani zoyenera kuzipewa pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku [sg-CN tsa. 56 ndime 9]
32. Mavalidwe athu angatigwirizanitse ndi gulu linalake la anthu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w72 tsa. 666.]
33. Kuyamikira chifundo cha Yehova kungasonkhezere munthu kulamulira mtima ndi kukwirira zophophonya. [w98-CN 11/1 tsa. 6 ndime 3]
34. Ndi mwayi waukulu kwambiri kuchereza ndi kutumikira modzichepetsa atumiki okhulupirika a Yehova amene ali mu utumiki wapadera. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 11/1 tsa. 31 ndime 1.]
35. Munthu woopa Mulungu amayesetsa kukwaniritsa malonjezo ake a kubweza ngongole zake, ngakhale kuti zinthu zina zosayembekezeka zingapangitse kuti kubweza ngongoleyo kukhale kovuta kusiyana ndi mmene amalingalilira. [w98-CN 11/15 tsa. 27 ndime 1]