Zotsatira Zolimbikitsa za m’Munda
‘Ndidziŵa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye, namwe, nawone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.’ (Mlal. 3:12, 13) Mawu a Mfumu Solomo ameneŵa akugogomezera mmene munthu amasangalalira ‘kuona zabwino m’ntchito zake.’ Inde, dzinja likayamba kulima ndi kubzala chimanga imakhala “ntchito” yaikulu, koma si mmene zimakhalira ‘bwino’ kuona mbewu zambiri nthaŵi yokolola.
Yesu mu fanizo lake lina anati, “munda ndiwo dziko lapansi.” Izi n’zoona pankhani yobzala ndi kukulitsa mbewu za choonadi cha Baibulo. Kupitiriza kulalikira ena ndi “ntchito” yaikulu. ‘Timagwira “ntchito” yaikulu polalikira anansi athu, anzathu, achibale athu, anzathu akusukulu ndi akuntchito. Cholinga chathu chimakhala kubzala mbewu za choonadi m’maganizo ndi m’mitima yawo mwa kuwagaŵira magazini ndi mabuku ena ofotokoza za m’Baibulo. Timagwira “ntchito” yaikulu popanga maulendo obwereza ndiponso poyesetsa kuyamba nawo maphunziro a Baibulo. Komatu timasangalala kwabasi ‘kuona zabwino m’ntchito zathu,’ ena akalabadira choonadi chifukwa chakuti tinali “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.
Dziko la Malaŵi ndi gawo la ‘munda wa dziko lapansi.’ Malipoti aposachedwapa akusonyeza kuti, m’Malaŵi munonso, anthu a Mulungu akulimbikira “ntchito.” Malipoti a theka la chaka chino chautumiki akusonyeza kuti, pa avareji ofalitsa okwanira 46,629 ankapita mu utumiki wakumunda mwezi uliwonse. Imeneyi yaposa avareji ya chaka chatha ndi anthu pafupifupi 6 pa anthu 100 alionse. Mwezi wa February unali mwezi umene kwanthaŵi yoyamba ofalitsa tinapitirira 47,000, popeza anthu amene anapereka malipoti anali 47,098. Mu February tinagaŵiranso magazini ambiri kwa anthu achidwi kuposa nthaŵi za m’mbuyomo. Tinagaŵira magazini okwana 127,091. Tinagaŵiranso mabuku ndi mabulosha ambiri. Izi zikusonyeza kuti tingathe kuyambitsa maphunziro a Baibulo ambiri! Mu February, tinachititsa maphunziro a Baibulo 37,385. Kodi titenga nthaŵi yaitali motani kuti tifike 40,000? Tingathe kumachititsa maphunziro ambiri chonchi ndi anthu achidwi ngati tibwerera kwa onse amene anasonyeza chidwi ndiponso ngati mitu ya mabanja itamachititsa maphunziro a Baibulo a banja nthaŵi zonse. Kenako, tidzakhala ndi antchito ambiri m’munda.—Mat. 9:37, 38.
Tikulimbikira “ntchito” ndipo ‘tikuona zabwino’ za m’munda. Pitirizani kugwira ntchito yabwino, abale ndi alongo. Ngati tipitiriza ‘kuoka ndiponso ‘kuthirira’ mwanjira imeneyi, tidzakhala otsimikiza kuti Yehova adzapitiriza ‘kukulitsa’ mbewu.—1 Akor. 3:6, 7.