Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/01 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 12/01 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi mpingo ukaitanitsa mabuku payenera kupita nthaŵi yaitali motani kuti uitanitsenso ena?

Mabuku ophunzirira Baibulo amathandiza kwambiri pofalitsa uthenga wabwino, ndipo ife monga ofalitsa, tikulimbikitsidwa kuwagwiritsa ntchito kwambiri mu utumiki. Njira yosavuta yogaŵira mabuku mwa chopereka chaufulu imene inayamba mu January 2000, yathandiza mipingo yonse kuitanitsa mabuku ndi magazini okwanira mwezi uliwonse. Tsopano mipingo yonse iziitanitsa mabuku mwezi ndi mwezi m’malo modikira kuti alandire kaye mabuku amene anaitanitsa kale ndiyeno n’kuitanitsa ena.

Mipingo ina ikuitanitsa panthaŵi imodzi mabuku okwanira kugwiritsa ntchito kwa miyezi ingapo kuti isamaitanitse mwezi ndi mwezi. Chonde musachite zimenezi. M’malo mwake, tikulimbikitsa mipingo yonse kuti iyambe kutumiza Fomu Yofunsira Mabuku mwezi uliwonse, pofika tsiku loyamba la mwezi uliwonse. Mwa njira imeneyi, nthaŵi zonse mpingo uzilandira mabuku mwezi ndi mwezi, ndipo mipingo sidzafunikira kusungira mabuku ambiri. Pochita zimenezi n’kofunika kulemba bwino mabuku amene mwaitanitsa n’kusunga zimene mwalembazo ndiponso kuchitiratu zimenezi mukudziŵa kuti mudzagwiritsa ntchito mabukuwo patapita miyezi itatu kuyambira pamene mwaitanitsa. Zili choncho chifukwa chakuti pamapita miyezi itatu kuti mulandire mabukuwo.

Poganizira zimenezi, Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi uliwonse pa “Zilengezo,” umatiuziratu mabuku amene tidzagaŵira m’miyezi itatu yakutsogolo. Amachita zimenezi n’cholinga chofuna kuonetsetsa kuti mukulalikira mwadongosolo ndiponso mokwanira m’gawo lanu lonse. Mwachitsanzo, mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno muona kuti sanangosonyeza mabuku ogaŵira mu December mokha ayi, komanso mu January, February ndi March.

Kuneneratu mabuku amene tidzagaŵira m’miyezi ya kutsogolo kumachititsa kuti mpingo udziŵiretu nthaŵiyo isanafike. Zimenezi zimathandiza kuti mpingowo uitanitse mabuku pa nthaŵi yabwino podziŵa kuti mukaitanitsa mabuku ku nthambi, pamatenga miyezi itatu kuti mulandire. Pachifukwa chimenechi, mpingo wanu poitanitsa mabuku mu December muno muyenera kuphatikizanso chogaŵira cha March chimene ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Oda yanu ya January iyenera kuphatikizapo chogaŵira cha April. Chitaninso chimodzimodzi m’miyezi yotsatira. Mwezi uliwonse, woyang’anira wotsogolera azikonza chilengezo choti chiperekedwe kumpingo asanaitanitse mabuku n’cholinga choti mwina abale ndi alongo angaitanitse mabuku amene akufuna kugwiritsa ntchito paokha ndiponso mu utumiki. Tiyenitu tonsefe tigwiritse bwino ntchito mabuku athu ophunzirira Baibulo kuti tithandize kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu ndi kulemekeza dzina lokwezeka la Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena