Anthu Achimwemwe Kwambiri Padziko Lapansi
1 “Odala [“Achimwemwe,” NW] anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Sal. 144:15) Mawu ameneŵa akutchula Mboni za Yehova kukhala anthu achimwemwe kwambiri padziko lapansi. Palibe chimwemwe chachikulu choposa chimene chimadza ndi kutumikira Mulungu yekha woona ndi wamoyo, Yehova. Popeza ndi “Mulungu wachimwemwe,” om’lambira amasonyezanso chimwemwe. (1 Tim. 1:11, NW) Kodi ndi mbali ziti za kulambira kwathu zimene zimatipangitsa kukhala achimwemwe kwambiri?
2 Chifukwa Chake Tili Achimwemwe: Yesu anatitsimikizira kuti chimwemwe chimabwera mwa ‘kuzindikira zosoŵa zathu zauzimu.’ (Mat. 5:3) Timachita zimenezi mwa kupitiriza kuphunzira Baibulo ndiponso kupezeka pa misonkhano yathu yonse yachikristu. Kuphunzira choonadi cha Mawu a Mulungu kwatimasula ku bodza ndi zolakwa za chipembedzo. (Yoh. 8:32) Malemba atiphunzitsanso mmene tingakhalire bwino pa moyo wathu. (Yes. 48:17) Chifukwa cha zimenezi, timasangalala ndi mayanjano abwino achikristu m’gulu lathu la abale achimwemwe.—1 Ates. 2:19, 20; 1 Pet. 2:17.
3 Timapeza chimwemwe chochuluka mwa kumvera malamulo apamwamba a Mulungu a makhalidwe abwino, popeza timadziŵa kuti izi zimatiteteza ndipo zimasangalatsa Yehova. (Miy. 27:11) Mtolankhani wa nyuzipepala ina anati: “Ngakhale kuti Mboni za Yehova zili ndi malamulo okhwima, zimasangalala kwambiri. Ana komanso achikulire [m’gululi] amaoneka achimwemwe kwabasi ndiponso osatekeseka.” Kodi ndi motani mmene tingathandizire ena kukhala achimwemwe ngati ife?
4 Thandizani Ena Kupeza Chimwemwe: Dziko ladzaza ndi mavuto, ndipo anthu ambiri alibe chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo. Koma, ife tili ndi tsogolo labwino, timadziŵa kuti tsiku lina mavuto adzakhala nthano chabe. (Chiv. 21:3, 4) Choncho, timachita utumiki mwachangu, kufunafuna anthu oona mtima amene tingawauze chiyembekezo chathu ndi zikhulupiriro zathu ponena za Yehova.—Ezek. 9:4.
5 Mlongo wina amene ndi mpainiya anati: “Palibe chosangalatsa kuposa kuthandiza anthu kudziŵa Yehova ndi choonadi chake.” Tiyeni tichite zonse zimene tingathe polimbikitsa anthu ambiri kuvomera phunziro la Baibulo lapanyumba. Kutumikira Yehova ndiponso kudzipereka kuthandiza ena kuti am’tumikire kumabweretsa chimwemwe chachikulu.—Mac. 20:35.