Kubereka Ana Mwanzeru—Udindo Wachikristu—Gawo 2
1 Masiku ano ntchito yofunika kwambiri padziko lapansi ndi ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Choncho, ndi bwino kwa Akristu kudzifunsa momwe kupeza banja kapena kubereka ana, ngati ali kale pa banja, kudzakhudzire zimene amachita mu ntchito yofunika imeneyi.
2 Tili mu “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu loipa limene lili pafupi kuwonongedwa. Mtumwi Paulo analosera kuti “masiku otsiriza” a dongosolo la Satana adzakhala “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Pofuna kusonyeza kuti kulera ana kukakhala chimodzi mwa zinthu zoŵaŵitsa, iye anawonjezera kuti ana adzakhala “osamvera akuwabala.” Iye ananena kuti anthu, kuphatikizapo ana ndi achinyamata omwe, adzakhala “osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe.” (2 Tim. 3:1-3) Mikhalidwe yofala imeneyi imapangitsa kulera ana kukhala kovuta kwambiri kwa Akristu, monga mmene anthu ambiri aonera.
3 Zonsezi zikusonyeza kuti m’pofunika kuganiza bwino pankhani yobereka ana. N’zoona kuti kubereka ana kumasangalatsa kwambiri, koma kungabweretsenso mavuto ambiri. Kuli ndi ubwino ndi kuipa kwake. Ndi udindo wa munthu aliyense kusankha kuti akufuna kubereka ana angati, ndipo ena sayenera kutsutsa zimene anzawo asankha. Koma ayenera kusankha mogwirizana ndi malangizo a Baibulo. Pa 1 Timoteo 5:8, mtumwi Paulo anati: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye.” Udindo wa m’Malemba wakuti munthu azisamalira bwino banja lake ndi waukulu kwambiri. Chimodzi mwa zimene zingapangitse kuti munthu athe kusamalira bwino banja lake ndi kukula kwa banjalo. Makolo angavutike kusamalira bwino banja lawo ngati banjalo n’lalikulu kwambiri. Ndi udindo wa makolo achikristu kupezera ana awo chakudya chokwanira, zovala zokwanira, malo ogona abwino ndi thandizo la kuchipatala lokwanira. Kukondadi ana awo kudzathandiza anthu okwatirana kuona momwe zinthu zilili m’dziko limene tikukhala ndiponso kuzindikira kuti kulera ana masiku ano ndi ntchito yovuta.
4 Chifukwa cha zimenezi, Akristu ena okwatirana asankha kusabereka. Ena asankha kusabereka ana ambiri. Chotero ambiri amasankha kapena kukonza kuti banja lawo lidzakhale lalikulu motani m’malo mongolekerera zinthu kumachitika ndi kukhala ndi ana ambirimbiri mpaka pomwe adzalekere kubereka poganiza kuti zonse zidzayenda bwino. (Luka 14:28) Choncho, okwatirana ena popeŵa kubereka ana ambiri amene sangathe kuwasamalira bwino, asankha kugwiritsa ntchito njira za kulera. Komabe, pankhani imeneyi, pamabwera funso lofunika kwambiri lakuti, kodi Akristu ayenera kuiona motani nkhani ya kulera? Tidzakambirana zimenezi mu nkhani yakuti “Kubereka Ana Mwanzeru—Udindo Wachikristu—Gawo 3.”