Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tiyenera kukumbukira chiyani poŵerenga ndime pamisonkhano?
Nthaŵi yambiri ya Phunziro la Nsanja ya Olonda ndiponso ya Phunziro la Buku la Mpingo imathera kuŵerenga ndime. Izi zikutanthauza kuti mbale woŵerenga amakhala ndi udindo waukulu wophunzitsa. Ayenera kuŵerenga mopereka ‘tanthauzo’ la nkhaniyo kuti omvetserawo aimvetse ndiponso iwakhudze mtima. (Neh. 8:8) N’chifukwa chake, woŵerenga afunikira kukonzekera bwino ntchito yakeyi. (1 Tim. 4:13; onani phunziro 6 la Buku Lolangiza la Sukulu.) Nazi zina mwa mfundo zimene zimafunika kuti munthu aŵerenge bwino pamaso pa anthu.
Tsindikani Poyenera Kutero: Dziŵiranitu mawu ofunika kutsindika kuti apereke tanthauzo loyenera.
Tchulani Mawu Molondola: Kuti omvetsera azindikire mawu amene mukuŵerengawo, n’kofunika kuwatchula bwino.
Lankhulani Mokweza ndi Mwamphamvu: Kulankhula mokweza ndiponso mwamphamvu kumapatsa munthu chidwi, kumakhudza mtima ndiponso kumalimbikitsa womvetsera.
Ŵerengani Mosaopseza Anthu Ndiponso Monga Mukukambirana Nkhani: Kuti munthu aŵerenge mmene amalankhulira sayenera kudodomadodoma. Woŵerenga akakonzekera mokwanira amakhala womasuka, ndipo amaŵerenga mosangalatsa osati mogwetsa ulesi ndiponso motopetsa.—Hab. 2:2.
Ŵerengani Zimene Zalembedwa: Nthaŵi zambiri mawu am’munsi ndiponso mawu a m’mabulaketi (mkutiramawu) amaŵerengedwa mokweza ngati akutanthauzira mawu osindikizidwawo. Koma mawu ongosonyeza kumene kwachokera nkhaniyo saŵerengedwa. Mawu am’munsi ayenera kuŵerengedwa pamene pali chizindikiro chake m’ndimemo, mwa kuyamba ndi mawu akuti: “Mawu am’munsi akuti . . . ” Mukatha kuŵerenga mawu am’munsi, ingopitirizani kumaliza kuŵerenga ndimeyo.
Kuŵerenga bwino pamaso pa anthu, ndi njira imodzi yabwino kwambiri imene ‘tingaphunzitsire ena kusunga zinthu zonse zimene analamula’ Mphunzitsi wathu Wamkulu.—Mat. 28:20.