Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 24, 2003. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 6 mpaka February 24, 2003. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
Luso la Kulankhula
1. Zoona Kapena Zonama: Kuti munthu aŵerenge molondola ayenera kuonetsetsa kuti zomwe zikuŵerengedwa zikumveka bwino, ngakhale zitasiyanako pang’ono ndi zimene zalembedwa. Fotokozani. [be-CN tsa. 83]
2. Perekani Mawu Oyenera M’mipata Yosalembedwayi: Kuti munthu aŵerenge molondola, iye ayenera _________________________ , _________________________ , _________________________ ndipo atero mokweza mawu. [be-CN tsa. 85]
3. N’chifukwa chiyani kulankhula momveka bwino kuli kofunika? (1 Akor. 14:8, 9) [be-CN tsa. 86]
4. Kodi zina mwa zinthu zomwe zingapangitse kuti kulankhula kusamveke bwino ndi ziti, ndipo kodi tingachite chiyani kuti tilankhule momveka bwino kwambiri? [be-CN mas. 87-8]
5. Kodi ndi mawu ena ati amene agwiritsidwa ntchito m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu m’miyezi iŵiri yapitayi omwe mumaona kuti amakuvutani kuwatchula molondola kapena mogwirizana ndi tanthauzo lake? [be-CN tsa. 92]
Nkhani Na. 1
6. Zoona Kapena Zonama: Maso athu angatithandize kumvetsera. Fotokozani. [be-CN tsa. 14]
7. Perekani Mawu Oyenera M’mipata Yosalembedwayi: Pofuna kuchita chipongwe Yesu, alembi ndi Afarisi akuuza anthu kuti: “Uyu _________________________ koma ndi mphamvu yake ya _________________________ , mkulu wa _________________________ .” [gt-CN Mutu 41 ndime 5]
8. Perekani Mawu Oyenera M’mipata Yosalembedwayi: Yesu anagogomezera unansi wake ndi ophunzira ake mwa kunena kuti: “Pakuti aliyense adzachita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba, yemweyo ndiye _________________________ wanga, ndi _________________________ wanga, ndi _________________________ wanga.” [gt-CN Mutu 42 ndime 9]
9. Kodi zitsanzo za Hana, Marko, ndi Eliya zingatithandize bwanji kupirira polefulidwa? Kodi tingazigwiritsire ntchito motani pothandiza ena? [w01-CN 2/1 mas. 20-3]
10. Kodi kuzindikira mipikisano ya maseŵera othamanga yomwe inkachitika kale kungatithandize motani kumvetsa bwino mavesi ena a m’Baibulo? Kodi zimenezo ziyenera kukhudza miyoyo yathu motani? [w01-CN 1/1 mas. 28-31]
Kuŵerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu
11. Zoona Kapena Zonama: Popeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, n’kosayeneranso kupemphera kuti, “Ufumu wanu udze.” (Mat. 6:10) Fotokozani. [be-CN tsa. 279; w96-CN 6/1 tsa. 31]
12. Zoona Kapena Zonama: Mawu a Yesu a pa Mateyu 11:24 amatanthauza kuti anthu omwe Yehova anawawononga ndi moto mu Sodomu ndi Gomora adzaukitsidwa. Fotokozani.
13. Sankhani Yankho Lolondola: Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene Yesu anam’tchula pa Mateyu 24:45-47 ndi (a) Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova; (b) kagulu ka Akristu onse odzozedwa okhala pa dziko lapansi panthaŵi iliyonse; (c) Yesu Kristu mwiniwakeyo. Kapolo ameneyu amapereka chakudya panthaŵi yake kwa “banja lake,” loimiridwa ndi (a) odzozedwa aliyense payekha; (b) nkhosa zina; (c) onse omwe amaŵerenga mabuku achikristu. Mbuye anakhazika kapolo ameneyu kuti ayang’anire zinthu zake zonse m’chaka cha (a) 1914; (b) 33 C.E.; (c) 1919.
14. Sankhani Yankho Lolondola: Khoka lomwe Yesu anatchula m’fanizo lake pa Mateyu 13:47-50 limaphatikizapo mpingo wa Akristu odzozedwa ndi (a) Ufumu Waumesiya wa Mulungu; (b) anzawo a nkhosa zina; (c) Chikristu Chadziko.
15. Malinga ndi mawu a Yesu a pa Mateyu 5:24, kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwazindikira kuti mwalakwira wolambira mnzanu? [g96-CN 2/8 mas. 14-5]