Khalani Chitsanzo pa Ntchito Zabwino
1. N’chifukwa chiyani tifunika kusamala kwambiri khalidwe lathu pa msonkhano wachigawo?
1 Tikasonkhana anthu ambiri pa misonkhano yachigawo, zochita zathu ndiponso mmene timachitira zinthu ndi anthu ena zimaonekera kwambiri kwa anthu otiona. Motero, aliyense wa ife afunika kutsatira kwambiri langizo la m’Baibulo lakuti: ‘Khala wodziletsa; m’zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino.’ (Tito 2:6, 7) Pangafunike khama lalikulu kuti ‘tisapenyerere zathu za ife tokha, koma kupenyereranso za anzathu.’ (Afil. 2:4) Tiyeni tione mbali zina zimene tingagwiritsire ntchito langizo limeneli pa Msonkhano Wachigawo umene ukubwerawu wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero.”
2. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya malo ogona?
2 Malo Ogona: Nthaŵi zambiri, abale amadzipezera okha malo ogona ndipo amakhala ndi achibale kapena anzawo m’mizinda imene mukuchitikira misonkhano yachigawo. M’madera a kumidzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’misasa yaikulu imene anthu ongodzipereka pa msonkhanopo amamanga. Pa misonkhano ina yochepa, anthu amagona m’nyumba zogonamo za sukulu. Ngati tikukhala ndi abale kapena achibale athu, si bwino kuti tipezerepo mwayi pa kuolowa manja kwa abale amene akutisungawo poganiza zokhala kunyumbako masiku enanso msonkhano utatha kuti tichiteko tchuthi. Malo ameneŵa ndi oti tikhaleko nthaŵi ya msonkhano yokhayo basi. Anthu amene akusungidwa pa nyumbapo ayenera kuonetsetsa kuti iwo ndi ana awo azichita zinthu mwaulemu m’nyumba ya munthu amene akuwasungayo ndipo asaononge chilichonse kapena kugwiragwira katundu ndiponso kupita kuzipinda zina m’nyumbamo. Ngati eninyumba apeza mavuto ena alionse pankhani imeneyi, nthaŵi yomweyo ayenera kuuza Dipatimenti yoona za Malo Ogona ku msonkhano, ndipo abale a m’dipatimenti imeneyi adzakhala okondwa kukuthandizani.
3, 4. Kodi ana angatamanditse bwanji Yehova, ndipo kodi makolo ali ndi udindo wotani?
3 Makolo ndi Ana: M’dziko lino limene ana ambiri ndi opanda khalidwe, ana athu amaoneka kuti ndi osiyana, ndipo zimenezi zimatamanditsa Yehova ndi gulu lake. Komabe, nthaŵi zina pabuka mavuto pamene ana sanayang’aniridwe bwino. (Miy. 29:15) Makolo sayenera kusiya ana ali okhaokha pa malo a msonkhano.
4 Makolo ena aona kuti zimathandiza kukambirananso ndi ana awo msonkhano usanafike za khalidwe limene amafunika kusonyeza. (Aef. 6:4) Amathandiza ana awo kumvetsa kuti chikondi chenicheni chachikristu “sichichita zosayenera” ndiponso “sichitsata za mwini yekha.” (1 Akor. 13:5) Msonkhano wachigawo ndi nthaŵi imene yapatulidwa kuti tiphunzitsidwe ndi Yehova, ndipo ana, ngakhalenso akulu, angasonyeze kulemekeza dongosolo limeneli mwa khalidwe lawo pamsonkhanopo ndiponso pena paliponse.—Yes. 54:13.
5. Kodi khalidwe lathu labwino lingakhudze bwanji ena?
5 Khalidwe lathu labwino lingathandize kwambiri kuthetsa maganizo olakwika amene anthu ena amakhala nawo ndipo lingakopere anthu ku kulambira koona. (Mat. 5:16; 1 Pet. 2:12) Tiyeni tithandize onse amene tingakumane nawo pamsonkhano wathu wachigawo kuti alandire umboni wabwino poona zochita zathu ndi mmene tikuchitira nawo zinthu. Mwa njira imeneyi ‘tidzadzionetsera tokha chitsanzo cha ntchito zabwino’ ndipo tidzalemekeza Yehova.—Tito 2:7.
[Bokosi patsamba 4]
Ganizirani Ena
▪ M’ganizireni amene akukusunganiyo
▪ Yang’anirani bwino ana anu