Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/03 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 11/03 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu November: Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Ngati eninyumba ali nawo kale mabuku ameneŵa, gaŵirani bulosha lina lililonse. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe mungagaŵire Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Yandikirani kwa Yehova.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa December 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Akatha kuŵerengerako, mukalengeze kumpingo mutamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Mipingo iyambe kufunsira mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2003 pa oda yawo ya mabuku yotsatira. Mabaundi voliyumuŵa adzakhalapo mu Chingelezi ndi Chifalansa. Mabaundi voliyumuŵa azidzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo kufikira pamene adzayambe kupezeka ndi kutumizidwa. Mabaundi voliyumu ndi zinthu za oda yapadera.

◼ Zopereka za m’macheke zizilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.” Adiresi ya ofesi ya nthambi ndi Watch Tower Bible and Tract Society, P. O. Box 30749, LILONGWE 3. Macheke opita ku mpingo wanu azilembedwa kuti ndalamazo apatse mpingowo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena