Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/03 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 12/03 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu December: Lambirani Mulungu Woona Yekha. January: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Yandikirani kwa Yehova. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Ngati anthu ali nalo kale buku limeneli, tingagaŵire buku la Samalani Ulosi wa Danieli!

◼ Tikukumbutsa abale amene amasamalira maakaunti a mpingo kuti ndalama za m’mabokosi a Ntchito ya Padziko Lonse azizitumiza mwezi uliwonse ndipo asamagwiritse ntchito ndalama zimenezi monga zopereka za Nyumba ya Ufumu kapena kugulira zinthu zina za pampingopo.

◼ Mipingo iyenera kuitanitsa mapepala oitanira anthu ku Chikumbutso cha chaka chamaŵa pa fomu yawo Yofunsira Mabuku (S-14) yotsatira. Mapepalaŵa alipo mu Chicheŵa, Chingelezi, ndi Chitumbuka. Muyenera kuitanitsa m’mipukutu ya mapepala 100 m’chinenero chilichonse. Chonde itanitsani mosamala popeza kuti anapangira anthu achidwi okha basi, osati kugaŵira chisawawa.

◼ Dziŵani kuti Chikumbutso cha 2005 chidzachitika Lachinayi, pa March 24, dzuŵa litaloŵa. Taneneratu zimenezi kuti abale apezeretu maholo ena ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo ikufunika kupeza malo ena. Ngati zili choncho, akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo n’kutsimikizira kuti mwambowu usadzadodometsedwe ndi zochitika zina pamalowo kuti Chikumbutsocho chidzachitike mwamtendere ndi mwadongosolo. Popeza mwambowu ndi wapadera, posankha wokamba nkhani ya Chikumbutso, bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu yemwe alidi woyenerera, osati kungosinthana kapena kuti chaka chilichonse azingokamba mbale mmodzimodzi yemweyo. Ngati pali wodzozedwa amene ndi mkulu komanso angathe kukamba nkhaniyo musankheni ameneyo.

◼ Kuyambira pa March 15, 2004, mpaka pa May 16, 2005, pa Phunziro la Buku la Mpingo tidzayamba kuphunzira buku lakuti Yandikirani kwa Yehova. Mipingo imene ikufuna mabuku azilembo zazikulu iyenera kuitanitsa mabukuŵa mofulumira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena