Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu January: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Yandikirani kwa Yehova. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzachita zotheka kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Ngati anthu ali nalo kale buku limeneli, mungagaŵire buku la Samalani Ulosi wa Danieli! April: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, phatikizanipo opezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo mokhazikika. Yesetsani kugaŵira buku la Lambirani Mulungu. Tidzachite zotheka kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, makamaka ngati ena anamaliza kale kuphunzira buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji.
◼ Kuyambira mlungu wa March 15, 2004, tidzayamba kuphunzira buku la Yandikirani kwa Yehova pa Phunziro la Buku la Mpingo.
◼ Oyang’anira madera adzayamba kukamba nkhani ya onse yatsopano yakuti “Kodi Mumakonda Mfundo za Ndani za Chikhalidwe?” Adzayamba tsiku lililonse kuyambira February mpaka March 7.
◼ Mipingo ipange makonzedwe abwino odzachita Chikumbutso chaka chino Lamlungu, pa April 4, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumira, musayendetse zizindikiro za Chikumbutso kufikira dzuŵa litaloŵa. Funsani odziŵa za nyengo kwanuko kuti mudziŵe nthaŵi yoloŵera dzuŵa m’dera lanu. Popeza kuti tsiku limeneli sipayenera kuchitika misonkhano kupatulapo msonkhano wokonzekera utumiki wa kumunda, m’pofunika kusintha kuti Phunziro la Nsanja ya Olonda lidzakhaleko tsiku lina. Oyang’anira madera ayenera kusintha pulogalamu yawo ya misonkhano mlungu umenewu malinga ndi mmene zinthu zilili kumeneko. Ngakhale kuti ndi bwino ngati mpingo uliwonse ungamachite Chikumbutso pawokha, izi sizitheka nthaŵi zina. Ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mpingo umodzi kapena yoposerapo ingapeze malo ena odzagwiritsa ntchito tsikuli madzulo. Tikupereka malingaliro akuti, ngati kungatheke mapulogalamu akatha pazipita mphindi zosachepera 40 ena asanayambe, kuti onse apindule mokwanira. Ndipo zimenezi zimapereka mpata wocheza ndi alendo ndi kulimbikitsa atsopano amene ali ndi chidwi. Bungwe la akulu liyenera kupanga makonzedwe okomera mpingowo.