Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/04 tsamba 7
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 8/04 tsamba 7

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 30, 2004. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya July 5 mpaka August 30, 2004. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. Kodi tingafotokoze bwanji chifukwa cha chiyembekezo chathu “ndi chifatso ndi mantha”? (1 Pet. 3:15) [be-CN tsa. 192 ndime 2-4]

2. N’chifukwa chiyani timafunika kulankhula motsimikiza? (Aroma 8:38, 39; 1 Ates. 1:5; 1 Pet. 5:12) [be-CN tsa. 194]

3. Kodi kulankhula motsimikiza kumasonyezedwa motani? [be-CN tsa. 195 ndime 3–tsa. 196 ndime 4]

4. Kodi kusamala n’kutani, n’chifukwa chiyani kuli kofunika, ndipo kodi tingakhale bwanji osamala n’kukhalanso olimba nthaŵi imodzimodziyo? (Aroma 12:18) [be-CN tsa. 197]

5. Asanalankhule, kodi munthu wosamala amaganizira chiyani? (Miy. 25:11; Yoh. 16:12) [be-CN tsa. 199]

NKHANI NA. 1

6. Kodi mtundu wa nkhani zimene timakambirana ndi anthu komanso mmene timaphunzirira Baibulo zingasonyeze bwanji mlingo umene tapita patsogolo m’choonadi? [be-CN tsa. 74 ndime 3–tsa. 75 ndime 2]

7. Kodi ‘kuchita machawi’ kapena kuti, kuwombola nthaŵi, kumatanthauza chiyani, ndipo kodi tingachite bwanji zimenezo? (Aef. 5:16) [w02-CN 11/15 tsa. 23]

8. Kodi Malemba amasonyeza bwanji moonekeratu kuti anthu onse ndi ofanana pamaso pa Mulungu, ndipo kodi zimenezi ziyenera kukhudza bwanji utumiki wathu? [w02-CN 1/1 mas. 5, 7]

9. Kodi dzina lapadera la Mlengi, lakuti Yehova, n’lofunika motani? [w02-CN 1/15 tsa. 5]

10. Kodi n’chiyani chinapangitsa nsembe ya Abele kukhala “yoposa” ya Kaini, ndipo tingaphunzirepo chiyani pamenepa chokhudza “nsembe yakuyamika” imene timapereka? (Aheb. 11:4; 13:15) [w02-CN 1/15 tsa. 21 ndime 6-8]

KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. Kodi Levitiko 18:3 angatithandize bwanji kupeŵa kukhala ndi maganizo olakwika a chabwino ndi choipa? (Aefeso 4:17-19) (w02-CN 2/1 tsa. 29)

12. Kodi “mikate iŵiri” imene inali kuperekedwa ndi mkulu wa ansembe monga “nsembe yoweyula” panthaŵi ya Madyerero a Masabata (Pentekoste) inali kuphiphiritsira chiyani mwaulosi? (Lev. 23:15-17) [w98-CN 3/1 tsa. 13 ndime 21]

13. Pamlandu wachigololo ngati umene unalembedwa pa Numeri chaputala 5, kodi “m’chuuno” mwa mkazi wolakwa ‘munkawonda’ m’lingaliro lotani? (Num. 5:27) [w84 4/15 tsa. 29; it-2 tsa. 1094]

14. N’chifukwa chiyani Miriamu ndi Aroni anatsutsana ndi Mose chifukwa cha mkazi wake amene anali Mkusi? (Num. 12:1)

15. Kodi ‘buku la Nkhondo za Yehova’ linali chiyani? (Num. 21:14)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena