Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 27, 2004. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya November 1 mpaka December 27, 2004. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Tchulani njira imodzi mwa njira zabwino zimene tingakopere chidwi cha omvera athu tikamakamba nkhani. [be-CN tsa. 218 ndime 3]
2. Tchulani mbali zofunika zisanu za mmene tingakambire mawu omaliza mogwira mtima. [be-CN tsa. 221 ndime 1 mpaka 4]
3. Kodi tingaonetsetse motani kuti zimene tikunena n’zoona? [be-CN tsa. 224 bokosi]
4. Kodi tingachite chiyani kuti tionetsetse kuti nkhani zathu pa misonkhano zikulemekeza kwambiri mpingo monga “mzati ndi mchirikizo wa choonadi”? (1 Tim. 3:15) [be-CN tsa. 224 ndime 1 mpaka 4]
5. Kodi lemba la Miyambo 14:15 tingaligwiritse ntchito motani ngati tikukamba za zochitika za tsiku ndi tsiku, mawu ogwidwa, kapena zokumana nazo? [be-CN tsa. 225 ndime 1]
NKHANI NA. 1
6. Kodi kupepesa kochokera pansi pa mtima kumene kungatithandize ‘kuyanjana ndi mbale wathu’ kumaphatikizapo chiyani? (Mat. 5:23, 24) [w02-CN 11/1 tsa. 6 ndime 1 ndi 5]
7. Kodi lemba la 2 Mafumu 13:18, 19 limatiphunzitsa chiyani za mmene tingakwanitsire ntchito imene Mulungu watipatsa? [w02-CN 12/1 tsa. 31 ndime 1 ndi 2]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
8. N’chifukwa chiyani lamulo la Mulungu pa Deuteronomo 22:28, 29 linanena kuti mwamuna wachiisrayeli akagonana ndi namwali wosapalidwa ubwenzi anayenera kum’kwatira ndipo sanayenera kum’sudzula? [w89-CN 11/15 tsa. 31]
9. Tikamalingalira za mgwirizano umene anapanga mafumu amene Aisrayeli analimbana nawo, kodi ndi zochitika zotani zimene tikuziona masiku ano zomwe zikufanana ndi zimenezo? [w86-CN 12/15 tsa. 24 ndime 5]
10. M’malo molemba mawu asayansi ofotokoza za kayendedwe ka dziko pa Yoswa 10:13, kodi n’chiyani kwenikweni chimene Yoswa amafuna kunena? [w81 10/1 tsa. 5]
11. N’chifukwa chiyani Aisrayeli ankapatsa mlendo wa m’mudzimo kapena kugulitsa kwa mlendo nyama yakufa yosakhetsa mwazi imene iwo sanayenera kudya? (Deut. 14:21)
12. Kodi pa Deuteronomo 20:5-7 tikupezapo phunziro lotani?
13. N’chifukwa chiyani kutenga ‘mphero, ngakhale mwana mphero monga chikole’ anakuyerekezera ndi kutenga “moyo wa munthu”?
14. Popeza kuti Aisrayeli analetsedwa kudya mafuta alionse, kodi kudya “mafuta a ana a nkhosa” kunatanthauza chiyani? (Deut. 32:13, 14)
15. Kodi tchimo la Akani, lingafanane ndi tchimo liti masiku ano? (Yos. 7:1-26) [w86-CN 12/15 tsa. 22 ndime 20]