Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 28, 2005. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 3 mpaka February 28, 2005. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera kufufuza nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi tingatani kuti tizilankhula zomveka bwino kwambiri? [be-CN tsa. 226 ndime 1–tsa. 227 ndime 1]
2. Kodi ndi mawu a mtundu wanji amene angafunike kuwafotokoza bwino? [be-CN tsa. 227 ndime 2–tsa. 228 ndime 1]
3. Ndi njira yothandiza iti pokamba nkhani imene ingatithandize kuphunzitsa anthu omvera kaǹthu kena? [be-CN tsa. 231 ndime 1-3]
4. Kodi tingatani powerenga lemba lodziwika bwino kwa omvera athu kuti iwo aphunzirepo kanthu? [be-CN tsa. 231 ndime 4-5]
5. Kodi pangakhale zotsatirapo zotani ngati tilimbikitsa omvera athu kuika maganizo awo pa tsatanetsane wa nkhani zozolowereka za m’Baibulo? [be-CN tsa. 232 ndime 2-4]
NKHANI NA. 1
6. Kodi kuphunzitsa anthu kuti ‘aope Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake’ kumaphatikizapo chiyani? (Mlal. 12:13) [be-CN tsa. 272 ndime 3–tsa. 273 ndime 1]
7. Kodi anthu tingawathandize bwanji kudziwa mtundu wa Mulungu amene Yehova ali kuwonjezera pa kungodziwa dzina lake? (Yow. 2:32) [be-CN tsa. 274 ndime 3-5]
8. Kodi kudziwa za Yesu ndi kuchitira umboni za iye n’kofunika motani? (Yoh. 17:3) [be-CN tsa. 276 ndime 1]
9. Kodi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu ndiponso kumvetsa bwino Baibulo n’zogwirizana motani ndi kumvetsa mbali imene Yesu amachita pa chifuniro cha Mulungu? [be-CN tsa. 276 ndime 2]
10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupiriradi kuti Yesu Kristu ndi Mfumu? [be-CN tsa. 277 ndime 4]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi atate wa Abrahamu, Tera, anali munthu wolambira mafano? (Yos. 24:2)
12. Kodi Gideoni anali wosalimba mtima mokwanira moti sakanatha kukwanitsa zimene Yehova anamutuma? N’chifukwa chiyani mukuyankha choncho? (Ower. 6:25-27)
13. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa kuona mmene Gideoni analankhulira ndi anthu a fuko la Efraimu? (Ower. 8:1-3)
14. Kodi kukana kuchereza alendo kwa anthu a mu m’mzinda wa Gibeya kunatanthauza chiyani? (Ower. 19:14, 15)
15. Ngati ‘aliyense anachita chom’komera pamaso pake,’ kodi sizikutanthauza kuti panali chisokonezo pamenepa? (Ower. 21:25)