Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 25, 2005. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya March 7 mpaka April 25, 2005. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi gwero la mfundo za nkhani imene tikukonzekera kukakamba tingaligwiritse bwino ntchito motani, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? [be-CN tsa. 234 ndime 1-3, mabokosi]
2. Kodi tiyenera kutenga mfundo zochuluka motani m’gwero la nkhani imene tapatsidwa? [be-CN tsa. 234 ndime 4–tsa. 235 ndime 1]
3. Kodi mafunso tingawagwiritse ntchito bwanji pofuna kulimbikitsa kukambirana mu utumiki wa kumunda? (Mac. 8:30) [be-CN tsa. 236 ndime 2-5]
4. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mafunso pothandiza ophunzira Baibulo kugwiritsa ntchito ‘luntha lawo la kulingalira’? (Aroma 12:1, NW) [be-CN tsa. 238 ndime 1]
5. Kodi cholinga cha mafunso omwe ali pa Aroma 8:31, 32 ndi Yesaya 14:27 n’chotani? [be-CN tsa. 239 ndime 1-2]
NKHANI NA. 1
6. Kodi Kristu tingamuyale motani monga maziko pa ntchito yathu yopanga ophunzira? (1 Akor. 3:11) [be-CN tsa. 278 ndime 1-2]
7. Popeza kuti Yehova anapereka mphamvu zonse zolamulira kwa Mwana wake mu 1914, kodi timatanthauza chiyani tikamapemphera kuti, ‘Ufumu wanu udze’? (Mat. 6:9, 10) [be-CN tsa. 279 ndime 4]
8. N’chifukwa chiyani Akristu onse ayenera kukhala ndi chidwi chofuna kudziwa kuwerenga, nanga Yesu anasonyeza motani chitsanzo pa nkhaniyi? [w03-CN 3/15 tsa. 10 ndime 5; tsa. 12 ndime 2]
9. Kodi zitsanzo za Yosiya ndi Yesu zingawathandize bwanji achinyamata kupita patsogolo mwauzimu? [w03-CN 4/1 tsa. 8 ndime 3-4; tsa. 10 ndime 3]
10. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire Mulungu? (Miy. 3:5, 6) [w03-CN 11/1 tsa. 4 ndime 6-7]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. N’chifukwa chiyani Hana anapemphera kuti Yehova “adzapatsa mphamvu mfumu yake,” pamene mu Israyeli munalibe mfumu? (1 Sam. 2:10)
12. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa mfundo yakuti Aisrayeli anagonjetsedwa ngakhale kuti likasa la chipangano linali pakati pawo? (1 Sam. 4:3, 4, 10)
13. N’chifukwa chiyani lemba la 1 Mbiri 2:13-15 likunena kuti Davide anali mwana wamwamuna wachisanu ndi chiwiri wa Jese, pamene lemba la 1 Samueli 16:10, 11 likusonyeza kuti anali wachisanu ndi chitatu?
14. Kodi “mzimu woipa” umene unavutitsa Sauli n’chiyani? (1 Sam. 16:14)
15. Kodi zimene “Samueli” analosera kudzera mwa mizimu ku Endori zinali zolondola? (1 Sam. 28:16-19)