Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 27, 2006. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 2 mpaka February 27, 2006. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imatithandiza bwanji ‘kupereka nsembe yakuyamika Mulungu ndi kuvomereza dzina lake’? (Aheb. 13:15) [be-CN tsa. 5 ndime 3–tsa. 6 ndime 1]
2. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuwerenga molondola? [be-CN tsa. 83 ndime 1-5]
3. Tikamalankhula ndi kuphunzitsa, n’chifukwa chiyani kulankhula momveka bwino kuli kofunika kwambiri? [be-CN tsa. 86 ndime 1-6]
4. N’chifukwa chiyani kutchula mawu molondola kuli kofunika, ndipo tiyenera kuganizira mfundo ziti? [be-CN tsa. 89 ndime 1–tsa. 90 ndime 3, bokosi]
5. Kodi malangizo ena amene angatithandize kulankhula mosadodoma pokambirana ndi ati? [be-CN tsa. 94 ndime 4-5, bokosi]
NKHANI NA. 1
6. Kodi gulu la Mulungu n’lozikidwa pa chiyani? [od-CN tsa. 6 ndime 3]
7. Kodi mfundo yoti Mulungu ali ndi mbali yakumwamba ya gulu lake iyenera kutikhudza motani? [od-CN tsa. 8 ndime 3]
8. Kodi kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova kumaphatikizapo chiyani? [od-CN tsa. 9 ndime 4]
9. Kodi Yesu Kristu ali bwanji mutu wa gulu looneka la padziko lapansi? [od-CN tsa. 12 ndime 2]
10. Popeza Yesu Kristu ndi Mtsogoleri ndi Wolamulira wa anthu a Mulungu masiku ano, kodi tingasonyeze bwanji kuti tikuzindikira udindo wake pa makonzedwe a Mulungu? [od-CN tsa. 14 ndime 1-2]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi Urimu ndi Tumimu, amene anthu ankagwiritsa ntchito akafuna kudziwa yankho lochokera kwa Yehova, anagwiritsidwanso ntchito anthu atabwerako ku ukapolo? (Ezara 2:61-63)
12. N’chifukwa chiyani Ayuda ambiri ku Babulo sankafuna kubwerera ku Yerusalemu ndi Ezara? (Ezara 7:28–8:20)
13. Kodi ntchito yomanganso linga ikanagwirika bwanji ndi dzanja limodzi lokha? (Neh. 4:17, 18)
14. Popeza makalata achinsinsi nthawi zambiri ankawaika m’thumba lotsekedwa, n’chifukwa chiyani Sanibalati anatumiza “kalata wosatseka” kwa Nehemiya? (Neh. 6:5)
15. Kuwonjezera pa ‘kutsutsana’ ndi Ayuda amene anayambiranso kuchita zinthu zoipa, monga momwe anachitira m’mbuyomo ndi akulu ndi aufulu, kodi Nehemiya anachitanso chiyani pofuna kuwadzudzula? (Neh. 13:25, 28)