Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu a chidwi, kuphatikizanso amene amapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo, yesetsani kuwagawira buku latsopano la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Cholinga chathu chikhale kuyambitsa phunziro la Baibulo. June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, agawireni buku la Chimwemwe cha Banja. July ndi August: Mungathe kugwiritsa ntchito kalikonse ka timabuku ta masamba 32 totsatirati: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dikirani!, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha!
◼ Popeza kuti mwezi wa July uli ndi masiku a Loweruka asanu ndi a Lamlungu asanunso, udzakhala mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo pa June 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Mukatha kuwerengerako, lengezani kumpingo pamodzi ndi lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Macheke operekedwa pa msonkhano wachigawo a zopereka za ntchito ya padziko lonse ndiponso otumizidwa ku ofesi ya nthambi azilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.” Adiresi ya ofesi yoona za ndalama ya ku nthambi ndi iyi: Watch Tower Bible and Tract Society, Box 30749, Lilongwe 3.
◼ N’koyenera kuti mafomu ofunsira upainiya wokhazikika atumizidwe ku ofesi ya nthambi patatsala masiku osachepera 30 kuti lifike tsiku limene munthu wafuna kuyamba upainiyawo. Mlembi wa mpingo ayenera kuonetsetsa kuti mafomuwo alembedwa bwino malo onse. Ngati amene akufuna kuchita upainiyayo sakukumbukira tsiku limene anabatizidwa, angangolemba loyerekezera ndi kulisunga. Mlembi ayenera kulemba tsiku limeneli pa Khadi la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa (S-21).
◼ Tikupepesa chifukwa chosaika masiku a msonkhano wachigawo wa ku Ntcheu, dera la C-14, mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2006. Udzachitika pa September 1 mpaka 3, 2006.