Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, agawireni buku la Chimwemwe cha Banja. July ndi August: Mungathe kugwiritsa ntchito kalikonse ka timabuku ta masamba 32 totsatirati: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dikirani!, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha! September: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Yesetsani mwapadera kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo wanu woyamba. Bwererani kwa aliyense amene munam’gawira bukuli n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo la panyumba.
◼ Popeza kuti mwezi wa July uli ndi masiku a Loweruka asanu ndi a Lamlungu asanunso, udzakhala mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza.
◼ Nyimbo zotsatirazi zidzaimbidwa pa msonkhano wachigawo wa chaka chino: 8, 14, 19, 38, 40, 43, 59, 71, 74, 85, 91, 92, 106, 181, 195, 204, 207, ndi 212. Kuti anthu adzathe kuimba bwinobwino nyimbozi, tikulimbikitsa mipingo yonse kuphunzira nyimbo imodzi kapena ziwiri pambuyo pa msonkhano uliwonse.
◼ Taona kuti pa misonkhano yachigawo komanso pa misonkhano yachikristu ya mpingo, anthu ena amakhalabe pansi poimba nyimbo za Ufumu. Tikukulimbikitsani nonse kuimirira poyimba nyimbo zotamanda Yehova chifukwa chakuti imeneyi ndi mbali ya kulambira Yehova.
◼ Ofesi ya nthambi yasiya kutumiza ku mipingo timatumba toikamo zopereka zaufulu. Ngati munatumiza kale ndalama ku ofesi ya nthambi zoitanitsira timatumba timeneti, tidzakubwezerani ndalama zanu.
◼ Mabuku Atsopano amene alipo:
Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Lazilembo zazikulu—Chichewa
◼ Ma CD Atsopano amene alipo:
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo—Chingelezi
Moyo wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere—Chingelezi
Mulungu Amafunanji?—Chingelezi
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako—Chingelezi
◼ Ma DVD Atsopano amene alipo:
Pursue Goals That Honour God—American Sign Language