Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu July ndi August: Mungathe kugwiritsa ntchito kalikonse ka timabuku ta masamba 32 totsatirati: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dikirani!, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha! September: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Yesetsani mwapadera kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo wanu woyamba. Bwererani kwa aliyense amene munam’gawira bukuli n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo la panyumba. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Munthu amene wasonyeza chidwi, muonetseni kabuku kakuti Dikirani! n’cholinga chokulitsa chidwi chomwe ali nacho pa zinthu za m’Baibulo.
◼ Kuyambira mwezi wa September, oyang’anira dera azidzakamba nkhani ya mutu wakuti: “Kodi Mbiri Yanu Ndi Yotani kwa Mulungu?”
◼ Kuyambira mlungu woyambira January 8, 2007, tidzayamba kuphunzira kabuku kakuti Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? pa Phunziro la Buku la Mpingo. Mipingo iwodetseretu timabuku tokwanira pasadakhale.
◼ N’koyenera kuti mafomu ofunsira upainiya wokhazikika atumizidwe ku ofesi ya nthambi patatsala masiku osachepera 30 kuti lifike tsiku limene munthu akufuna kuyamba upainiyawo. Mlembi wa mpingo ayenera kuonetsetsa kuti mafomuwo alembedwa bwino m’malo onse. Ngati amene akufuna kuchita upainiyayo sakukumbukira tsiku limene anabatizidwa, angangolemba loyerekezera ndi kulisunga. Mlembi ayenera kulemba tsiku limeneli pa Khadi la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa (S-21).
◼ Alembi a mipingo ayenera kuonetsetsa kuti ali ndi Kalata Yotsimikiza Kuikidwa kwa Mpainiya (S-202) ya mpainiya aliyense wokhazikika amene ali mu mpingomo. Ngati alibe, ayenera kudziwitsa ofesi ya nthambi
◼ Kuwerengera kwa chaka ndi chaka kwa mabuku ndi magazini onse amene ali m’sitoko kuchitike pa August 31, 2006 kapena tsiku lina lililonse loyandikana nalo, ndipo ziwonkhetso zonse muzizilemba pa fomu ya Kuŵerengera Mabuku (S-18). Chiwerengero cha magazini amene alipo mungachipeze kwa mtumiki wa magazini. Mlembi wa mpingo ayenera kuyang’anira kuwerengeraku. Iye pamodzi ndi woyang’anira wotsogolera afunikira kusaina fomuyi. Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-18). Chonde tumizani pepala loyambirira ku ofesi ya nthambi pasanadutse pa September 6. Sungani pepala lachiwiri m’faelo yanu. Pepala lachitatulo mungaligwiritse ntchito ngati lowonkhetserera.