Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/06 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 12/06 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu December: Gawirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ngati mpingo wanu uli nawo. January: Gawirani kabuku ka Dikirani! February: Gawirani buku la Yandikirani kwa Yehova. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire mabuku ena akale omwe mpingo wanu uli nawo ambiri. March: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo.

◼ Timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso cha 2007 titumizidwa posachedwa m’chinenero cha mpingo uliwonse. Ngati m’gawo lanu anthu amalankhula zinenero zina ndipo mukufuna timapepala m’zinenero zimenezo, muyenera kupempha timapepalati posachedwapa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Timapepalati tidzakhalapo m’Chichewa, Chingelezi, ndi Chitumbuka. Muitanitse zinenero zokhazo zimene zikufunika m’gawo lanu.

◼ Dziwani kuti Chikumbutso cha chaka cha 2008 chidzachitika Loweruka, pa March 22, dzuwa litalowa. Taneneratu zimenezi kuti abale apezeretu malo ena ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo pakufunika kupeza malo ena. Akapeza malo ena, akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo n’kutsimikizira kuti mwambowu sudzadodometsedwa ndi zochitika zina pamalowo. Popeza Chikumbutso ndi mwambo wapadera, bungwe la akulu posankha wokamba nkhani liyenera kusankha mmodzi mwa akulu omwe alidi oyenerera, osati kungosinthana kapena kuti chaka chilichonse azingokamba m’bale mmodzimodzi yemweyo. Ngati pali wodzozedwa amene ndi mkulu komanso angathe kukamba nkhaniyo, asankhe ameneyo.

◼ Mabuku Atsopano Amene Alipo:

Watch Tower Publications Index 2001-2005—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena