Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 7

Zilengezo

◼ January: Gawirani buku la Chidziŵitso kapena kabuku ka Dikirani! February: Gawirani buku la Yandikirani kwa Yehova. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire mabuku ena akale omwe mpingo wanu uli nawo ambiri. March: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pa misonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.

◼ Kuyambira mu February mpaka kufika pa March 4, mutu wa nkhani ya onse ya oyang’anira madera udzakhala wakuti “Kodi Ndani Adzakhale Oyenera Kulowa M’dziko Latsopano la Mulungu?”

◼ Mipingo iyenera kukonzekera bwinobwino kudzachita Chikumbutso chaka chino Lolemba, pa April 2, dzuwa litalowa. Nkhani ya Chikumbutso ingathe kuyamba msanga koma musayambe kuyendetsa zizindikiro mpaka dzuwa litalowa. Mverani zimene odziwa zanyengo anene zokhudza nthawi imene dzuwa lidzalowere kwanuko. Mpingo uliwonse uyenera kuyesetsa kuti ukhale ndi mwambo wake wa Chikumbutso. Komabe, nthawi zina zimenezi sizingatheke. Ngati m’Nyumba ya Ufumu imodzi mumasonkhana mipingo ingapo, mpingo umodzi kapena mipingo inayo idzapeze malo ena ochitirako Chikumbutso. Ngati n’kotheka, pofuna kuti mipingo yonse ipindule ndithu ndi macheza, pazitha mphindi zosachepera 40 mpingo wotsatira usanayambe mwambo wawo wa Chikumbutso. Bungwe la akulu liyenera kukonza dongosolo lokomera mpingowo.

◼ Alembi a mipingo ayenera kuonetsetsa kuti ali ndi Kalata Yotsimikiza Kuikidwa kwa Mpainiya (S-202) ya mpainiya aliyense wokhazikika amene ali mu mpingomo. Ngati alibe, ayenera kudziwitsa ofesi ya nthambi polemba kalata.

◼ Mipingo yambiri imatumiza mochedwa khadi la lipoti la utumiki wa mwezi ndi mwezi (S-1) ku ofesi ya nthambi. Tikukumbutsa alembi kuti aziyesetsa kuti pofika pa 6 mwezi wotsatira malipotiwa azikhala atatumizidwa.

◼ Ndife osangalala kulengeza kuti patulutsidwa DVD yatsopano m’Chingelezi ya mutu wakuti Organized to Share Good News and Whole Association of Brothers (dvjwa). Tsopano mipingo ingathe kuitanitsa DVD imeneyi pa mafomu oitanitsira mabuku.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena