Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 3-4
  • Kudziwa Kulemba ndi Kuwerenga Pakati pa Anthu a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudziwa Kulemba ndi Kuwerenga Pakati pa Anthu a Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 3-4

Kudziwa Kulemba ndi Kuwerenga Pakati pa Anthu a Mulungu

1 Atumiki ambiri a Mulungu amene anatchulidwa m’Baibulo ankadziwa kuwerenga ndi kulemba. Petulo ndi Yohane, omwe anali atumwi a Yesu, anali asodzi achiyuda koma analemba mabuku a m’Baibulo mu Chigiriki, osati m’chinenero chawo cha ku Galileya. Olemba Baibulo ena amene anachita chimodzimodzi, ndi Davide yemwe anali mbusa ndiponso Yuda, mng’ono wake wopeza wa Yesu, yemwe mwina anali kalipentala. Yobu ankatha kuwerenga ndi kulemba, ndipo buku la m’Baibulo lotchedwa dzina lake limasonyeza kuti ankadziwa zina ndi zina zokhudza sayansi. Ayeneranso kuti anali ndi luso la zolembalemba, chifukwa mawu ake amene ali m’buku la Yobu analembedwa mwandakatulo.

2 Pakati pa Aisiraeli, amene anali kudziwa kuwerenga ndi kulemba sanali atsogoleri a mtundu wokha. Malangizo opatsidwa kwa Aisiraeli oti ‘azilemba’ malamulo a Mulungu pamphuthu za nyumba zawo anasonyeza kuti anthuwo anali odziwa kulemba ndi kuwerenga, ngakhale kuti n’zoonekeratu kuti kulemba kotchulidwa m’malangizowa kunali kophiphiritsira. Amosi anali oweta nkhosa, ndipo Mika anali mneneri wa kumidzi; komabe, anthu awiri onsewa analemba mabuku a m’Baibulo. (Deut. 6:8, 9; Amosi 1:1; Mika 1:1) Yesu anali ndi ufulu wowerenga mipukutu yonse youziridwa ya Malemba a Chiheberi m’masunagoge, ndipo nthawi ina, ali m’sunagoge anawerengera anthu lemba n’kusonyeza mmene lembalo linali kunenera za iyeyo. Atumwi akenso ankadziwa kuwerenga ndi kulemba ndipo anagwira mawu ndi kutchula Malemba a Chiheberi kambirimbiri m’mabuku ndi makalata amene analemba.—Luka 4:16-21; Mac. 17:11.

3 Maphunziro N’ngofunika kwa Akhristu: Popeza Mulungu wapereka Mawu ake olembedwa, amafuna kuti olambira ake adziwe bwino kulemba ndi kuwerenga mmene angathere. Kumvetsa bwino pamene tikuwerenga Baibulo kumathandiza kuti tisamavutike kugwiritsa ntchito uphungu wa m’Baibulowo. N’zoona kuti mbali zosiyanasiyana za m’Baibulo tiyenera kuziwerenga kangapo kuti tithe kumvetsa mfundo zake ndi kuti tithe kuzisinkhasinkha.—Sal. 119:104; 143:5; Miy. 4:7.

4 Chaka chilichonse, anthu a Yehova amalandira zowerenga zambiri zothandiza, ndipo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi amene amayang’anira ntchito yokonza zowerenga zimenezi. (Mat. 24:45-47) Mabuku ndi magazini amenewa amafotokoza nkhani zokhudza banja, miyambo yosiyanasiyana, zipembedzo, sayansi, ndi nkhani zina zambiri. Koma chofunika kwambiri n’chakuti amakhala ndi malangizo a m’Malemba pankhani zauzimu. Ngati Mkhristu satha kuwerenga, nkhani zofunika kwambiri zingathe kumupita ndipo mwina sangathe kukwanitsa ngakhale utumiki wake m’dera lomwe wapatsidwa.—2 Tim. 4:5.

5 Kuphunzira Kuwerenga: Pofuna kuthandiza anthu m’njira imeneyi, Mboni za Yehova zakonza ntchito yothandiza anthu kudziwa kuwerenga ndi kulemba ndipo zikuchita ntchitoyi kudzera m’mipingo yawo, komanso pophunzitsa anthuwo pawokhapawokha. Padziko lonse, zaphunzitsa amuna ndi akazi osawerengeka. M’Malawi mokha muno, kuyambira mu September 2005 mpaka August 2006 Mboni za Yehova zathandiza anthu pafupifupi 1,000 kudziwa kuwerenga ndi kulemba. Ndithudi, mipingo imene ili ndi makalasi ophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba tiyenera kuiyamikira.

6 Komabe, oyang’anira madera ena amapereka malipoti akuti m’mipingo ina anasiya kuphunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba. Mwachitsanzo, madera awiri amene tikaphatikiza mipingo yake ikukwana 40, asiya kuphunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba. M’dera lina lomwe lili ndi mipingo 25, mipingo iwiri yokha ndi imene inali ndi ndondomeko ya nthawi zonse yothandiza anthu osatha kuwerenga ndi kulemba. Kodi mipingo inayo inasiiranji kuphunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba? Kodi tingati tsopano aliyense mumpingomo amadziwa kuwerenga? Kapena kodi anthu amene sadziwa kuwerenga ndi kulemba anagwa ulesi chifukwa chakuti amene anaikidwa kuti aziwaphunzitsa sabwerabwera?

7 Tikulimbikitsa mipingo imene ikufunika kuthandiza anthu osadziwa kuwerenga ndi kulemba omwe amapezeka pa misonkhano ya mipingoyo kuti iyambe makalasi amenewa mwamsanga, pogwiritsa ntchito kabuku kakuti “Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba.” Kabukuka kalembedwa n’cholinga chothandiza munthu kudziwa zinthu zofunikira kwambiri kuti azitha kuwerenga ndi kulemba. Mungagwiritsenso ntchito mabuku ena ophunzirira, mogwirizana ndi mmene ophunzirawo akudziwira kuwerenga. Bungwe la Akulu liyenera kukonza makalasi omwe ayenera kuyang’aniridwa ndi Oyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Makalasiwa asachitike panthawi imene nkhani za ophunzira mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu zikukambidwa. Kuti muwathandize mokwanira, m’pofunikira nthawi yambiri kuposa imene ingapezeke panthawi ya Sukulu ya Utumiki. Akulu aone kuti pakufunika thandizo lotani mumpingo mwawo ndi kupeza nthawi yoperekera thandizoli. Malinga ndi thandizo limene likufunikira, akuluwo angakonze zoti kaya pakhale kalasi kapena angakonze zoti aziphunzitsa anthu enaake pawokhapawokha. Ophunzirawa akapita patsogolo ndithu, alimbikitseni kuti ayambe kumakamba nkhani za mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.

8 Pangafunikirenso mphunzitsi wodziwa bwino kuphunzitsa. Zingakhale bwino ngati mungapatse udindowo kwa mbale amene amawerenga bwino komanso amene amadziwa bwino chinenerocho. Ngati mbale woteroyo palibe, akulu angapemphe mlongo yemwe angakwanitse zimenezo komanso wachitsanzo chabwino. Mlongoyo ayenera kuvala chinachake kumutu pophunzitsa. (1 Akor. 11:3-10; 1 Tim. 2:11, 12) Asanayambe ntchitoyi, anthu amene apatsidwa ntchito yophunzitsa ayenera kuwerenga malangizo amene ali pa tsamba 3 la kabuku kakuti “Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba,” pa kamutu kakuti “Zokhudza Mphunzitsi.”

9 Makalasi ophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba asamaime. Musalole kuti makalasiwo aime mpaka onse ofuna kuthandizidwa atathandizidwa. Ndi bwino kuti mphunzitsi akhale ndi buku lolembamo mayina a anthu a m’kalasi yophunzira kuwerenga ndi kulemba ndipo azisunga mayina a anthu amene amabwera nthawi zonse. Izi zimathandiza akulu kudziwa mmene maphunzirowo akuyendera. Popeza ofesi ya nthambi imafunitsitsa kwambiri kuti abale ndi alongo athu azidziwa kulemba ndi kuwerenga, oyang’anira oyendayenda pochezera mipingo azionanso mmene makalasi ophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba akuyendera.

10 Mlengi wathu, Yehova Mulungu, mwachisomo anapatsa anthu nzeru zoti azitha kuphunzira kuwerenga ndi kulemba. Koma munthu sangapeze luso limeneli popanda khama. Mphoto yaikulu kwambiri ya kudziwa kuwerenga ndi kulemba ndiyo kutha kumvetsa Mawu a Mulungu ndi kumvera malangizo a Mulungu akuti: “Ulingiriremo usana ndi usiku.”—Yos. 1:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena