Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/07 tsamba 7
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 4/07 tsamba 7

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 30, 2007. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya March 5 mpaka April 30, 2007. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA LULANKHULA

1. Kodi tingatani kuti autilaini yathu ikhale yophweka?[be-CN tsa. 168 ndime 4]

2. Tchulani njira zinayi za mmene tingakambire nkhani m’njira yotsatirika. [be-CN tsa. 170 ndime 3 mpaka tsa. 172 ndime 4]

3. Ndi mfundo ziti zimene tiyenera kukumbukira pamene tikusankha mfundo zoti tiike m’nkhani yathu? [be-CN tsa. 173 ndime 1 ndi 2]

4. Kodi pali ubwino wotani wolankhula kuchokera mumtima? [be-CN tsa. 175 ndime 2 mpaka 4]

5. N’chifukwa chiyani kukamba nkhani mmene mumalankhulira ndi anthu n’kofunika, ndipo tingatani kuti tichite zimenezi? [be-CN tsa. 179 ndime 4, ndi bokosi; tsa. 180, bokosi]

NKHANI NA. 1

6. Kodi m’bale azikonzekera motani akapatsidwa mbali ya mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu? [be-CN tsa. 47 ndime 3 ndi 4]

7. Kodi n’chiyani chomwe chili chofunika kwambiri pa dipo la Khristu kuposa madalitso amene ifeyo timawapeza chifukwa cha dipo limeneli? [w05-CN 11/1 tsa. 14 ndime 1]

8. Kodi malemba olembedwa mu autilaini ya nkhani ya onse angagwiritsidwe ntchito motani pokamba nkhaniyi? [be-CN tsa. 53 ndime 1 ndi 2]

9. Kodi cholinga cha Yesu monga mphunzitsi chinali chiyani, ndipo tingam’tsanzire motani? [be-CN tsa. 57 ndime 1]

10. Pophunzitsa, n’chifukwa chiyani kusiyanitsa zinthu kumakhala kothandiza? [be-CN tsa. 57 ndime 3 ndi 4]

KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. Kodi tingatsatire motani uphungu wopezeka pa Yeremiya 6:16 woti tiyende ‘m’mayendedwe a kale, mmenemo muli njira yabwino’?

12. N’chifukwa chiyani Yehova anasankha chumba [“dokowe” NW] monga chophunzitsira Ayuda osakhulupirika, ndipo zimenezi zingatiphunzitse chiyani? (Yer. 8:7)

13. Kodi masiku ano, tingagwiritse ntchito motani uphungu wa pa Yeremiya 15:17 ponena za mmene timaonera zosangalatsa?

14. Kodi anthu ali ngati dothi m’dzanja la Woumba Wamkulu, yemwe ndi Yehova, m’njira yanji? (Yer. 18:5-11)

15. Kodi mndandanda wa mayiko omwe ali pa Yeremiya 25:17-26, ukusonyezanji masiku ano?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena