Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/07 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 7/07 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu July ndi August: Mungagwiritse ntchito kalikonse ka timabuku tamasamba 32 iti: Dikirani!, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kwambiri kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo wanu woyamba. Ngati mwininyumba ali nalo kale bukuli, mum’sonyeze mmene angapindulire nalo mwa kupanga naye mwachidule phunziro la Baibulo. October: Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani! Mukabwerera kwa anthu amene anachita chidwi, agawireni ndi kukambirana nawo za m’kapepala ka Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Chitani zimenezi ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.

◼ Mwezi wa September ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.

◼ Kuyambira mwezi wa September, oyang’anira dera azidzakamba nkhani ya mutu wakuti “N’chiyani Chimasonyeza Kuti Baibulo N’lodalirika?”

◼ N’koyenera kuti mafomu ofunsira upainiya wokhazikika atumizidwe ku ofesi ya nthambi patatsala masiku osachepera 30 kuti lifike tsiku limene munthu wafuna kuyamba upainiyawo. Mlembi wa mpingo ayenera kuonetsetsa kuti mafomuwo alembedwa bwino malo onse. Ngati amene akufuna kuchita upainiyayo sakukumbukira tsiku limene anabatizidwa, angangolemba loyerekezera ndi kulisunga. Mlembi ayenera kulemba tsiku limeneli pa Khadi la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa (S-21).

◼ Timapepala Tatsopano Timene Tilipo:

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa? (Kapepala Na. 16)—Chitonga

Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa? (Kapepala Na. 25)—Chitonga

Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? (Kapepala Na. 26)—Chitonga

◼ Ma DVD Atsopano Amene Alipo:

The Bible—A Book of Fact and Prophecy (dvbbl-DVC)—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena