Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 27, 2007. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya July 2 mpaka August 27, 2007. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30.
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi tingalemekeze bwanji anthu mu utumiki komanso mumpingo? [be-CN tsa. 192 ndime 2 mpaka 4]
2. Kodi chofunika n’chiyani kuti tizitha kulankhula motsimikiza? [be-CN tsa. 196 ndime 1 mpaka 3]
3. Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kukhala osamala polalikira? [be-CN tsa. 198 ndime 1 mpaka 5]
4. N’chifukwa chiyani kukhala osamala kumafuna kudziwa nthawi yoyenera kunena zinthu? (Miy. 25:11) [be-CN tsa. 199 ndime 1 mpaka 3]
5. Tingatani kuti mawu athu azimveka olimbikitsa? [be-CN tsa. 203 ndime 3 mpaka tsa. 204 ndime 1]
NKHANI NA. 1
6. Kodi ndi anthu otani amene (1) angamakhale ndi mbali mu Msonkhano wa Utumiki; ndi (2) angalembetse mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu? [od-CN tsa. 66 ndime 1, tsa. 68 ndime 1]
7. Tchulani khalidwe limodzi limene lingatithandize kupirira tikamaona kuti ena akutilakwira. [w-CN 05 6/1 tsa. 29 ndime 4]
8. Kodi yankho la Yesu kwa Asaduki amene anam’funsa za kuuka kwa akufa likutiphunzitsa chiyani? (Luka 20:37, 38) [be-CN tsa. 66 ndime 4]
9. Kodi muziyankha motani wophunzira Baibulo kapena wokhulupirira mnzathu akakufunsani zimene ayenera kuchita pankhani inayake? [be-CN tsa. 69 ndime 4 mpaka 5]
10. Kodi ‘kukhala watsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo’ kumaphatikizapo chiyani? (Aef. 4:23) [be-CN tsa. 74 ndime 4]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Pa Ezekieli 9:2-4, kodi munthu wovala bafuta akuimira ndani, nanga kuika chizindikiro pamphumi kukutanthauzanji? [w-CN 88 9/15 tsa. 14 ndime 18]
12. Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu akufanana bwanji ndi “aneneri opusa otsata mzimu wawowawo” otchulidwa pa Ezekieli 13:3? [w-CN 99 10/1 tsa. 13]
13. Kodi Aisiraeli ankayesa kutani ponena “mwambi” womwe uli pa Ezekieli 18:2, ndipo tingaphunzirenji pankhani yoti aliyense adzayankha mlandu pa zomwe wasankha kuchita? [w-CN 88 9/15 tsa. 18 ndime 10]
14. Kodi pamene Ezekieli anakhala “chete” kapena kuti “wosalankhula” pamene mzinda wa Yerusalemu unazingidwa ndi kuwonongedwa zinatanthauza chiyani? (Ezek. 24:27; 33:22) [w-CN 03 12/1 tsa. 29]
15. Kodi “Gogi wa ku dziko la Magogi” ndani, nanga ndi liti pamene adzaukira mwamphamvu anthu a Yehova? (Ezek. 38:2, 16) [w-CN 97 3/1 tsa. 14 ndime 1 mpaka tsa. 15 ndime 3]