Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/07 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 11/07 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu November: Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, agawireni kabuku ka Dikirani! December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire buku la Yandikirani kwa Yehova kapena la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. January: Dikirani! February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

◼ Mwezi wa December ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.

◼ Tili ndi mabuku ambiri ofotokoza za Baibulo omwe anapangidwa kuti agwire ntchito polalikira anthu a zikhalidwe ndiponso zipembedzo zosiyanasiyana. Mtumiki wa mabuku ali ndi m’ndandanda wa mabuku othandiza amenewa.

◼ Macheke a zopereka za ntchito ya padziko lonse otumizidwa ku ofesi ya nthambi, azilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.” Adiresi ya ofesi yoona za ndalama ya ku nthambi ndi iyi: Watch Tower Bible and Tract Society, P. O. Box 30749, Lilongwe 3.

◼ Ofalitsa onse amene sanasaine Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA), akulimbikitsidwa kusaina makadiwa. Khadi limeneli limakutetezani kuti musathiridwe magazi. Akulu adzakuthandizani pamene mukufunika thandizo.—Onani mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006.

◼ Ofalitsa asamaperekenso lipoti la phunziro lililonse la Baibulo limene achititsa mwezi umenewo pogwiritsa ntchito mafomu a Lipoti la Phunziro (S-3). Komabe, pa Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4) azilembapo nambala ya maphunziro a Baibulo amene ali nawo padanga loyenera. Kuyambira panopa, mafomu a S-3 ntchito yake ingokhala yolembapo chiwerengero cha anthu ofika pa misonkhano.

◼ Nthawi zambiri zilengezo zofunika zonena za mmene tingaitanitsire mabuku zimalembedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Mtumiki wa mabuku ayenera kuzidziwa bwino zilengezo zimenezi akangolandira Utumiki Wathu wa Ufumu kuti athe kuzigwiritsa ntchito mwamsanga.

◼ Tikufuna kukumbutsa ofalitsa kuti pamafunika ndalama zambiri popanga mabuku a anthu osaona. Mabuku akuluakulu amafuna ndalama zambiri. Choncho, ndi mwayi wathu kuti tizipereka ndalama tikamatenga zinthu zimenezi. Mlembi wa mpingo akamavomereza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) ayenera kudziwa kuti zinthu zimenezi ndi za ofalitsa kapena maphunziro a Baibulo opita patsogolo. Ayenera kusonyeza pa fomuyi kuti waona bwinobwino zimene munthu waitanitsa ndipo wavomereza kuti zibwere. Amene analembetsa kuti azitumiziridwa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’zilembo za anthu osaona ayenera kudziwa ndalama zimene zimalowa popanga zinthu zimenezi.

◼ Mipingo iyambe kuitanitsa nyimbo zokonzedwanso za Kingdom Melodies—On Compact Disc, Volume 5 (cdm-5).

◼ Ma Compact Disc Atsopano Amene Alipo:

Yesetsani Kukwaniritsa Zolinga Zimene Zimalemekeza Mulungu—On Compact Disc (cdpsg)—Chichewa

Kodi Mumagonjera Ulamuliro wa Ndani?—Pa Compact Disc (cdsa)—Chichewa

◼ Ma DVD Atsopano a M’zinenero Zosiyanasiyana Amene Alipo:

Young People Ask—How Can I Make Real Friends?—On DVD (dvfe-DVC)—Chiarabu, Chidatchi, Chingelezi, Chimalagase, Chipwitikizi (cha ku Brazil), Chipwitikizi (cha ku Ulaya) ndi Chisipanishi (Pa DVD imodzi)

Organized to Share Good News and Whole Association of Brothers—On DVD (dvjwa-DVC)—Chiarabu, Chidatchi, Chingelezi, Chimalagase, Chipwitikizi (cha ku Brazil), Chipwitikizi (cha ku Ulaya) ndi Chisipanishi (Pa DVD imodzi)

To the Ends of the Earth and United by Divine Teaching—On DVD (dvedt-DVC) ili m’zinenero izi: Chiarabu, Chidatchi, Chingelezi, Chipwitikizi (cha ku Brazil), Chipwitikizi (cha ku Ulaya) ndi Chisipanishi (Pa DVD imodzi). DVD imeneyi yalowa m’malo mwa mavidiyo awiri a To the Ends of the Earth (vcea) ndi United by Divine Teaching (vcun) chifukwa choti mavidiyo amenewa tinasiya kupanga. Mipingo ingayambe kuitanitsa DVD yatsopano imeneyi.

◼ Ma Compact Disc a MP3 Atsopano Amene Alipo:

Bible Dramas—MP3 (mpdrm)—Chingelezi

◼ Makaseti Atsopano Amene Alipo:

Yesetsani Kukwaniritsa Zolinga Zimene Zimalemekeza Mulungu—Pa Kaseti (cspsg)—Chichewa

Lemekezani Ulamuliro wa Yehova—Pa Kaseti (csru)—Chitumbuka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena