Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 31, 2007. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya November 5 mpaka December 31, 2007. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30.
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi ndi mfundo zotani zimene tiyenera kukumbukira kuti mawu athu omaliza akhale ogwira mtima? [be-CN tsa. 221 ndime 1 mpaka ndime 5]
2. Kodi tingakhale bwanji otsimikiza kuti zonse zimene tikunena muutumiki wa kumunda n’zolondola? [be-CN tsa. 223 ndime 2 mpaka 4]
3. Kodi nkhani zathu pamisonkhano ya mpingo zingasonyeze motani kuti timalemekeza kwambiri mpingo monga “mzati ndi mchirikizo wa choonadi”? (1 Tim. 3:15) [be-CN tsa. 224 ndime 1 mpaka 4]
4. N’chifukwa chiyani kutsimikizira kuti zonena zathu n’zolondola kuli kofunika, ndipo tingachite bwanji zimenezi? [be-CN tsa. 225 ndime 1 ndi 2]
5. Kodi tingachite chiyani kuti anthu ena asamavutike kumva nkhani zathu tikamaphunzitsa? [be-CN tsa. 226 ndime 3 mpaka tsa. 227 ndime 1]
NKHANI NA. 1
6. N’chifukwa chiyani Akhristu odzipereka ndiponso anthu achidwi amapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Khristu? [od-CN tsa. 76 ndime 1]
7. Kodi tiyenera kuchita chiyani tisanauze wophunzira Baibulo kuti apite nafe muutumiki wa kumunda, ndipo n’chifukwa chiyani? [od-CN tsa. 79 ndime 1 mpaka 3]
8. Kodi akulu angadziwe bwanji kuti mwana ali ndi zomuyenereza kukhala wofalitsa wosabatizidwa? [od-CN tsa. 82 ndime 2]
9. Kodi ndani ayenera kupereka lipoti la utumiki wa kumunda powerengera mphindi 15 zilizonse m’malo mwa maola athunthu? [od-CN tsa. 87 ndime 1]
10. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyerekezera utumiki wathu wa kumunda ndi wa munthu wina? [od-CN tsa. 90 ndime 2]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi ulosi wa Yoweli wonena za tizilombo timene tinakwerera dziko unakwaniritsidwa motani m’nthawi ya atumwi, ndipo ukukwaniritsidwa motani masiku ano? (Yow. 2:1-10, 28) [w07-CN 10/1 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoweli ndi Amosi”]
12. Kodi “mtanga wa zipatso zamalimwe” ukutanthauzanji? (Amosi 8:1, 2) [w07-CN 10/1 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoweli ndi Amosi”]
13. Kodi Yehova “analeka” motani ‘choipa adachinena kwa Anineve,’ ndipo zimenezi ziyenera kutikhudza motani? (Yona 3:10) [w03-CN 7/15 tsa. 17 ndi 18]
14. Kodi kuyenda m’dzina la Yehova kumatanthauzanji? (Mika 4:5) [w03-CN 8/15 tsa. 17, ndime 19]
15. Kodi Yehova anabwera liti ku “kachisi” wake masiku ano kudzaweruza, ndipo panakhala zotsatirapo zotani? (Mal. 3:1-3) [w04-CN mas. 16 ndi 17 ndime 15 mpaka 18]