Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire buku lakuti Yandikirani kwa Yehova kapena lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. January: Gawirani kabuku kakuti Dikirani! February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
◼ M’bale amene woyang’anira wotsogolera wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo a miyezi ya September, October, ndi November. Munthu mmodzimodzi asawerengere maakaunti maulendo awiri otsatizana. Mukatha kuwerengerako, lengezani ku mpingo pamodzi ndi lipoti lotsatira la maakaunti.—Onani Malangizo Oyendetsera Maakaunti a Mpingo (S- 27).
◼ Dziwani kuti Chikumbutso cha chaka cha 2009 chidzachitika Lachinayi, pa April 9, dzuwa litalowa. Taneneratu zimenezi kuti abale apezeretu malo ena ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo pakufunika kupeza malo ena. Akapeza malo ena, akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo n’kutsimikizira kuti mwambowu sudzadodometsedwa ndi zochitika zina pamalowo.
◼ Mipingo ingayambepo kuitanitsa Watchtower Library—2007. CD imeneyi ili m’gulu la zinthu zofunsira mwapadera. Anaipangira ofalitsa ndipo timailandirira pa mpingo wa kwathu. Si yogawira kwa anthu ena kapena anthu amene angosonyeza chidwi ndi Mboni za Yehova. Maoda a CD ya 2006 amene tinalandira kale tidzawasintha kukhala a CD ya 2007. CD imeneyi ili mu Chingelezi ndi Chifalansa.
◼ Dziwani kuti Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku wa zilembo zazikulu wa 2008 (eslp08) ali m’gulu la zinthu zofunsira mwapadera, choncho sadzatumizidwa mwa njira imene titumizire Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku wa nthawi zonse wa 2008 (es08), m’malo mwake mipingo iyenera kuitanitsa.
◼ Ma DVD atsopano amene alipo:
Pursue Goals That Honor God—On DVD (dvpsg)—Chingelezi
Respect Jehovahˈs Authority—On DVD (dvru)—Chinenero chamanja cha ku America
Warning Examples for Our Day—On DVD (dvwx)—Chinenero chamanja cha ku America
(Zapitirizidwa patsamba 7)
Zilengezo (Zachokera patsamba 5)