Kodi Kukhala Munthu Wodzipereka kwa Mulungu Kumatithandiza Kuchita Zotani?
1. Kodi Yesu anasonyeza kudzipereka kwake kwa Mulungu m’njira yapadera yotani?
1 Yesu anasonyeza kudzipereka kwake kwa Mulungu m’njira zapadera zosiyanasiyana. Njira imodzi inali mwa ‘kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.’ (Luka 4:43) Atabatizidwa mu Yorodano chaka cha 29 C.E., Yesu anatha zaka zitatu ndi theka akugwira modzipereka ntchito yofunika kwambiri imeneyi. Iye anati ‘cholinga chimene anabwerera’ chinali kudzagwira ntchito imeneyi. (Maliko 1:38; Yoh. 18:37) Koma kodi zimenezi zinasonyeza motani kudzipereka kwake?
2, 3. Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Yesu kudzipereka kwambiri pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa? (b) Kodi n’chifukwa chiyani utumiki wa Yesu wolalikira ndi kuphunzitsa unali umboni wa kudzipereka kwake kwa Mulungu?
2 Kukhala munthu wodzipereka kwa Mulungu kumatanthauza kukhala ndi moyo wom’sangalatsa chifukwa cha kum’konda ndi kuyamikira makhalidwe ake abwino. Koma kodi n’chiyani chinalimbikitsa Yesu kudzipereka kwambiri pantchito yolalikira ndi kuphunzitsa m’zaka zomalizira za moyo wake padziko lapansi? Kodi iye anagwira ntchito imeneyi kungofuna kukwaniritsa udindo wake? Ayi. Chifukwa chimodzi chinali chakuti ankakonda anthu. (Mat. 9:35, 36) Komanso anali kudziwa bwino lomwe kuti anadzozedwa ndi mzimu woyera ndi cholinga choti akwaniritse utumiki wake. (Luka 4:16-21) Koma panalinso chifukwa china chimene chinamulimbikitsa.
3 Usiku womaliza wa moyo wake padziko lapansi pano, iye anauza atumwi ake momveka bwino kuti: “Ndimakonda Atate.” (Yoh. 14:31) Iye anali ndi chikondi chimenechi chifukwa chodziwa bwino kwambiri makhalidwe a Yehova. (Luka 10:22) Mtima woyamikira ndiponso wozindikira makhalidwe a Yehova ndi umenenso unalimbikitsa Yesu kukhala wokondwa pochita chifuniro cha Mulungu. (Sal. 40:8) Kuchita chifuniro cha Mulungu kunali “chakudya” chake, kutanthauza kuti kunali kofunika kwambiri pamoyo wake ndiponso kosangalatsa. (Yoh. 4:34) Iye anatisiyira chitsanzo chabwino pa “kufuna ufumu choyamba” m’malo motsogoza zofuna za moyo wathu. (Mat. 6:33) Chimene chikusonyeza kuti Yesu anali wodziperekadi kwa Mulungu kwenikweni si zimene anachita mu utumiki wake wolalikira ndi kuphunzitsa kapena kuchuluka kwa zimene anachitazo, koma makamaka zifukwa zimene anachitira utumikiwu.
4. Kodi n’chifukwa chiyani kungochita nawo utumiki si umboni wokwanira wakuti ndife wodzipereka kwa Mulungu?
4 Kodi tingatsatire bwanji Yesu monga “chitsanzo” chathu pankhani imeneyi? (1 Pet. 2:21) Aliyense amene akulabadira kuitana kwa Yesu kwakuti “bwera, ukhale wophunzira wanga” akulandira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Luka 18:22; Mat. 24:14; 28:19, 20) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kungolengeza uthenga wabwino, ndiye kuti ndife wodzipereka kwa Mulungu? Osati kwenikweni. Ngati tichita utumiki wathu mwamwambo chabe, kapena ndi cholinga chongokondweretsa achibale athu kapena anthu ena, sitinganene kuti utumikiwo ndi ‘ntchito ya kudzipereka kwa Mulungu.’—2 Pet. 3:11.
5. (a) Kodi chifukwa chachikulu chochitira utumiki chiyenera kukhala chiyani? (b) Ngati timachita utumiki wathu chifukwa chokonda kwambiri Mulungu, kodi zotsatirapo zake zimakhala zotani?
5 Mofanana ndi Yesu, zifukwa zathu zochitira utumikiwu ziyenera kukhala zoposa zimenezi. Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse [kutanthauza malingaliro ndi zokhumba za munthu], ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse [nzeru zonse za munthu], ndi mphamvu zako zonse.” Mlembi wina woganiza bwino anati zimenezi “n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.” (Maliko 12:30, 33, 34) Choncho zimene timachita n’zofunika, koma zifukwa zimene timachitira zinthuzo ndiye zofunika koposa. Chifukwa chachikulu cha zimene tikuchita mu utumiki chizikhala chakuti timakonda kwambiri Mulungu. Tikamatero, sitidzachita utumiki mwamwambo chabe koma tidzakhala ofunitsitsa kusonyeza kuti ndife odzipereka kwambiri kwa Mulungu mwa kuchita zonse zimene tingathe. (2 Tim. 2:15) Komanso tikamachita utumiki chifukwa chokonda Mulungu, sitidzakhala ndi mtima wokhalira kuyerekezera utumiki wathu ndi wa ena.—Agal. 6:4.
6. Kuti tipindule kwambiri ndi chitsanzo cha Yesu, kodi tiyenera kuchita chiyani?
6 Tikuyamikira kwambiri kuti Yehova watiululira chinsinsi chopatulika cha mmene tingakhalire anthu odzipereka kwa iye. Mwa kuphunzira mosamalitsa ndi kuchita zimene Yesu ananena komanso kuyesetsa kumutsanzira, tidzatha kukhala ndi moyo wosonyeza kuti ndife wodzipereka kwambiri kwa Mulungu. Monga Akhristu odzipereka ndi obatizidwa, Yehova adzatidalitsa kwambiri ngati titengera chitsanzo cha Yesu chokhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu.—1 Tim. 4:7, 8.