Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tidzayesetse mwapadera kupita kwa anthu amene angoyamba kumene kusonyeza chidwi, amene anafika pa Chikumbutso ndiponso pa nkhani yapadera, koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zambiri. Cholinga cha maulendowa chidzakhale kuyambitsa phunziro la Baibulo ndi anthu amene sanayambebe kuphunzira. June: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. July ndi August: Mungagwiritse ntchito kabuku kalikonse mwa timabuku tamasamba 32 iti: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi What Happens to Us When We Die?
◼ Chaka chautumiki chinayamba ndi kale, koma pali malipoti ambiri amene sitinalandirebe. Ngati mpingo wanu unalephera kutumiza malipoti a utumiki wa kumunda ku ofesi ya nthambi, chonde tumizani mwamsanga malipotiwo kuti lipoti lolondola lidzatumizidwe ku Bungwe Lolamulira.
◼ N’zosaiwalika! Tsiku la December 2, 2007, linali lapadera m’Malawi. Ophunzira 24 ochokera m’madera osiyanasiyana a dziko lino anamaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki yomwe inachitika m’Chingelezi mom’muno m’Malawi. Imeneyi ndi kalasi yoyamba kuchitikira m’Malawi muno. Sukuluyi ili ku Lilongwe pafupi ndi ofesi ya nthambi. Kalasi yachiwiri ya Chingelezi inayamba pa January 31, 2008. Kodi ndani angayenerere kupita ku sukuluyi? Pakali pano sukuluyi ili m’Chingelezi. Komabe, pali makonzedwe odzakhala ndi sukuluyi m’Chichewa. Zonse zikangoti zakonzeka, sukuluyi izidzachitika m’Chichewa. Choncho pakali pano, abale osakwatira amene amalankhula bwino Chingelezi ndipo akhala akulu kapena atumiki othandiza kwa zaka zotsatizana zosachepera ziwiri, angafunsire sukuluyi. Ndipo ayenera kukhala ndi zaka zoyambira 23 mpaka 62. Maphunziro a ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndi njira imodzi yothandizira akulu ndi atumiki othandiza osakwatira kukhala okonzeka kusenza maudindo owonjezereka m’mpingo ndi kuchita mautumiki ena. Choncho ndi mwayi waukulu kupita ku sukuluyi. Motero tikulimbikitsa abale kukalamira sukulu ya milungu 8 imeneyi.
◼ Mabuku Atsopano Amene Alipo:
Watch Tower Publications Index 2007 (dx07)—Chingelezi
◼ Ma DVD Atsopano Amene Alipo:
Acts of Apostles (dvAc)—Chinenero cha Manja cha ku America