Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/08 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 7/08 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu July ndi August: Mungagwiritse ntchito kabuku kalikonse mwa timabuku tamasamba 32 iti: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo paulendo woyamba. Ngati eninyumba ali nalo kale bukuli, athandizeni kuona mmene angapindulire nalo mwa kuwasonyeza mwachidule mmene timachitira phunziro la Baibulo. October: Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati munthu ali ndi chidwi, gawirani ndi kukambirana kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.

◼ Mwezi wa August ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.

◼ Kuyambira mwezi wa September, oyang’anira dera azidzakamba nkhani ya mutu wakuti, “Yendani mu Umphumphu.”

◼ Ofesi ya nthambi silembera ofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Woyang’anira wotsogolera azikonza zoti pazikhala chilengezo mwezi uliwonse asanatumize ku ofesi ya nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze m’bale woyang’anira za mabuku. Kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera.

◼ Kumbukirani izi: Mpaka pano m’chaka chautumiki chino, pali malipoti oposa 90 amene sitinalandirebe kuchokera ku mipingo ina. Tikukulimbikitsani kutumiza mwamsanga malipoti amenewa ku ofesi ya nthambi.

◼ Mipingo iyenera kuitanitsa mafomu okwanira a chaka chautumiki cha 2009 pa oda yotsatira. Musaitanitse mafomu otsatirawa chifukwa tidzakutumizirani limodzi ndi mtokoma wa mafomu apachaka: Lipoti la Mpingo (S-1), Maenvulopu a Lipoti (rce), Fomu Yofunsira Mabuku (S-14), Fomu Yotumizira Zopereka (S-20), Lipoti la Kuwerengera Maakaunti a Mpingo (S-25), Pepala la Maakaunti (S-26), Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205), Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b), Maoda a Magazini (M-202) ndi Lipoti la Maakaunti a Mpingo la Pamwezi (S-30). Mipingo iitanitse mafomu amene sanatchulidwe pamwambapa pogwiritsa ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Gwiritsani ntchito mafomu onse pa ntchito yokhayo imene anapangidwira.

◼ Mafomu a pachaka a chaka chautumiki cha 2009 atumizidwa posachedwa ku mpingo uliwonse m’maenvulopu aakulu.

◼ Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani liyenera kugwiritsidwa ntchito kuyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo osati kabuku ka Mulungu Amafunanji. Mungapitirize kugawira kabuku ka Mulungu Amafunanji mu utumiki wa kumunda mpaka pamene kadzatheretu m’sitoko.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zomwe Zilipo:

Watch Tower Publications Index 2007 (dx07)—Chinenero cha Manja cha ku America

◼ Ma CD Atsopano a MP3 Omwe Alipo:

Live With Jehovah’s Day in Mind (mpjd)—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena