Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/08 tsamba 3-4
  • Kuthandiza Ofalitsa Osakhazikika ndi Ofooka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Ofalitsa Osakhazikika ndi Ofooka
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 7/08 tsamba 3-4

Kuthandiza Ofalitsa Osakhazikika ndi Ofooka

1 Tili ndi chifukwa chabwino chothandizira ena kugwira nawo ntchito yolalikira pamlingo wokwanira ndithu malinga ndi mmene mikhalidwe yathu ingatilolere. Ena mwa ife ali ofalitsa odumphadumpha, ndipo zimenezi n’zodetsa nkhawa kwambiri. Kodi n’chiyani chingam’pangitse munthu kulola mwezi wathunthu kutha popanda kugwira nawo ntchito yofunika yolalikira ndi kupanga ophunzira?

2 Mwina ena anali kudwala kwambiri, ndipo enanso ankafuna kudzalowa mu utumiki wakumunda pakati pamwezi, ndiyeno n’kupeza kuti akumana ndi mikhalidwe ina yosayembekezereka, n’kuwalepheretsa kupita ku utumiki. Ena angakhale asakudziwa kuti utumikiwu uli chuma chimene tiyenera kuchisamala choyamba. (2 Akor. 4:7) Chinthu china chimene chakhala chofooketsa ndicho mavuto ochititsidwa ndi mwamuna kapena mkazi ndi achibale ena. Kulephera kuchita phunziro laumwini ndi kupezeka pamisonkhano nthawi zonse kwafooketsanso ena, moti akuiwala kuti mapeto a dziko la Satana akuyandikira msanga. (2 Pet. 3:11) Kanthu kena kagwetsa mtima wawo mphwayi. Iwo sakulankhulanso monga mwa kusefukira kwake. (Mat. 12:34) Kaya chifukwa chake n’chotani, koma afunikira kuthandizidwa.

3 Zimene Akulu Angachite: Akulu ayenera kuyesetsa kudziwa mikhalidwe ya onse mumpingo ndi zosowa zawo kuti akhoze kuwathandiza mwachikondi. Pakukumana kwawo akulu azizindikira wofalitsa aliyense amene wayamba kudumphadumpha ndi kuona kuti ndani amene angawathandize ndi mmenenso wothandizayo angachitire zimenezo. Mwinanso angalitchule vutolo polongosola zosowa za pampingo pa Msonkhano wa Utumiki. Mlembinso, podzaza makhadi a Cholembapo Ntchito za Wofalitsa cha Mpingo, ayenera kumazindikira umboni uliwonse wosonyeza kuti wofalitsa wayamba kudumphadumpha mu utumiki wakumunda.

4 Zimene Woyang’anira Phunziro la Buku Angachite: Mwezi uliwonse mlembi ayenera kupatsa woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo mpambo wa omwe amalephera kupereka lipoti la ntchito yakumunda, kuti athandizidwe msanga. Woyang’anira phunziroyo angawafikire mwaulemu amene ali odumphadumphawo kuti adziwe chimene chikuwapinga ndi mmene angawathandizire. (Miy. 27:23) Ambiri amene ali odumphadumpha adzayamikira atathandizidwa. Atadziwa mikhalidwe ya munthuyo, woyang’anira phunziroyo angalinganize kuti iyeyo agwire ntchito ndi munthuyo kapena kusankha wofalitsa wina wokhwima kapena mpainiya wina kuti atero. Zingathandizenso kuwapatsa anthu odumphadumphawo malingaliro othandiza ponena za kukonza ndandanda yoyenerana nawo malinga ndi mikhalidwe yawo. Kodi angakonzekere kugwira ntchito nthawi zonse mu utumiki wakumunda?

5 Pokachezera magulu a phunziro la buku, woyang’anira utumiki angalinganize zoti atengane ndi woyang’anira phunziro kuti akachezere anthu odumphadumpha. Choncho abale awiri okhwima adzakhoza kuthandizana kupereka uphungu ndiyeno n’kuthandiza anthu amenewo kumanga maziko onga thanthwe a kumvera lamulo la Khristu lakulalikira ndi kupanga ophunzira. Chotero iwo angasonkhezereke kumaika ntchito yolalikira patsogolo pa zinthu zawo zonse. (Aroma 10:10) Tiyeni tiyesetse kusonyeza kuti timakonda “achibale athu m’chikhulupiriro.”—Agal. 6:10.

6 Kuthandiza Ofooka: Limodzi mwa mafanizo a Yesu likunena za m’busa wosiya nkhosa 99 n’kukafunafuna imodzi yotayika. Kodi mukukumbukira zimene anati zidzachitika ngati imodzi yotayikayo inapezedwa? “Ndipo akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwera kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi 99 zosasochera zija.” (Mat. 18:13) Mipingo yambiri yakhala nacho chisangalalo choterocho pamene anthu ofooka anabwerera ku gulu lankhosa la Mulungu. Kodi mumpingo mwanu akalimo ena amene akhala ofooka m’zaka zaposachedwapa? Kodi mungatani kuti muwathandize?

7 Zimene Mungachite: Woyang’anira utumiki ndi mlembi amatsogolera kugwirizanitsa abale pakuyesayesa kuthandiza anthu ofooka. Akulu ayenera kulinganiza zochita zawo kuti oyamba akhale iwowo kukachezera anthuwo. Nthawi zina, mwina munthu wofookayo angakonde kuti wina azichita naye phunziro la Baibulo. Kapena wina amene ankaphunzira ndi munthuyo poyamba kapena wina amene munthuyo amadziwa ndi kumlemekeza, angakhalenso wothandiza. Ngati lili banja lonse, mwina pangafunikire kupempha mkulu wina kapena mtumiki wotumikira wokhoza bwino kuti aziphunzira nawo. Mlongo wofooka angathandizidwe ndi mlongo wachidziwitso. Wachinyamata zingam’khalire bwino kuchita ndi mtumiki wotumikira wachinyamata kapena mpainiya waluso. Mwina woyang’anira utumiki angalangize kuti nkhani zakutizakuti kapena buku lonse liphunziridwe. Cholinga n’chakuthandiza. Woyang’anira utumiki angagwiritsire ntchito aliyense amene ali wokhoza bwino kuchita zimenezo.

8 Akulu ena aona kuti n’kopindulitsa kuti paulendo woyamba azipenda nkhani yakuti ‘Bwererani kwa Mbusa wa Miyoyo Yanu’ mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1982, (Chingelezi). Mungawasonyeze chifundo cha Yehova ndipo mungawasimbire nkhani za anthu ena amene anabwerera kwa Yehova. Ngati ali wachinyamata yemwe wakhala wofooka, nkhani yakuti ‘Bwezerani Mtima Wanu kwa Yehova’ mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1982, (Chingelezi), ingam’thandize. Kenako, mungalinganize zochita naye phunziro la Baibulo la nthawi zonse.

9 Ofalitsa amene apatsidwa udindo ndi mwayi woyang’anira maphunziro amenewo ayenera kuwasonyeza anthuwo kuti akukondwera nawo. Ayenera kuyanjana nawo. Kuwasonyeza kuti n’kofunika kupezanso mphamvu yauzimu. Athandizeni kuzindikira kuti Yehova, mwa chikondi chake, ndi kuwadera nkhawa, wakonza kuti iwo athandizidwe payekhapayekha kudzera mwa gulu lake.

10 Ngakhale kuti ofalitsa ena ndi ena adzapemphedwa kuthandiza anthu ofooka, zimenezo sizikutanthauza kuti enanso sangathe kuthandiza. Onse angachite bwino kumawapatsa moni anthuwo pamene akufika pa Nyumba ya Ufumu ndi kumakambitsirana nawo nkhani zolimbikitsa. Asonyezeni kuti timakondwa kukhala nawo ndi kutinso tikuyembekezera kuwaona akupitabe patsogolo. Chidwi chowalimbikitsa chimenechi tiyenera kupitiriza kuchionetsa pamene iwo akupitabe patsogolo. Zotsatirapo zabwino zakhalapo chifukwa cha kuthandizana koteroko.−Aef. 4:16.

11 Indedi, timasangalala tikamaona anthu omwe kale anali ofooka akumasonkhananso nafe ndi omwe anali osakhazikika tsopano akumagwira ntchito mu utumiki mwezi uliwonse. Zimenezi zili choncho makamaka kwa aja amene iwo eniwo anakhozapo kuthandiza anthu ena. Tikupempherera kuti Yehova adalitse moolowa manja khama lathu ‘pochitira zabwino’ omwe anali ofooka kapena odumphadumpha ndiponso omwe ali “achibale athu m’chikhulupiriro.”−Agal. 6:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena