Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo woyamba. Ngati eninyumba ali nalo kale bukuli, athandizeni kuona mmene angapindulire nalo mwa kuwasonyeza mwachidule mmene timachitira phunziro la Baibulo. October: Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati munthu ali ndi chidwi, gawirani ndi kukambirana kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Zambiri za Baibulo? n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. November: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati anthu anena kuti ali ndi ana, agawireni buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.
◼ Mwezi wa November ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa chakuti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya 2009 ya panyengo ya Chikumbutso idzakambidwa mlungu woyambira April 20, 2009. Tidzalengeza mutu wa nkhaniyi m’tsogolo muno. Mipingo imene idzakhale ikuchezeredwa ndi woyang’anira dera kapena idzakhale ndi msonkhano mlungu umenewo, idzakhale ndi nkhani yapaderayi mlungu wotsatira. Mpingo uliwonse usadzakhale ndi nkhani yapaderayi usanafike mlungu woyambira April 20.
◼ Mipingo iyambe kuitanitsa mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2008, Watch Tower Publications Index 2008 ndiponso Watchtower Library—2008 Edition ya pa CD-ROM pafomu yawo yotsatira yofunsira mabuku. Zinthu zimenezi zili m’Chingelezi. Kumbukirani kuti Watchtower Library—2008 Edition inakonzedwera ofalitsa obatizidwa ndi osabatizidwa ndipo mungaiitanitse kudzera kumpingo basi. Ofalitsa amene amagwiritsa ntchito kwambiri Watchtower Library ndipo sagwiritsanso ntchito mabaundi voliyumu, angachite bwino kuganizira ngati angafunikebe kumaitanitsa mabaundi voliyumuwo.
◼ M’bale amene woyang’anira wotsogolera wam’sankha, awerengere maakaunti a mpingo a mwezi wa June, July, ndi August. Munthu mmodzi asawerengere maakaunti maulendo awiri otsatizana. Akatha kuwerengerako, lengezani ku mpingo lipotilo pambuyo pa lipoti lotsatira la maakaunti.—Onani Malangizo Oyendetsera Maakaunti a Mpingo (S-27).
◼ Tidzatumiza Lemba la Chaka cha 2009, choncho mipingo isaitanitse. Koma mipingo yatsopano, yokhazikitsidwa patadutsa pa September 1 idzafunika kuitanitsa zimenezi. Lemba la Chaka cha 2009 lidzakhalapo m’Chichewa, Chingelezi ndi Chitumbuka. Zinthuzi zimasindikizidwa ndi kampani yakunja, choncho tidzakumbukire kupereka ndalama zolipirira zimenezi. Mipingo ifunika kuika Lemba la Chaka cha 2009 podzafika pa January 1, 2009.
◼ Nthawi zina ofesi ya nthambi imalandira Mafomu Ofunsira Mabuku (S-14) ndi mafomu a Maoda a Magazini (M-202) opanda dzina la mpingo ndi nambala yake. Zikatero, sizitheka kukonza odayo. Choncho, tikukumbutsa mlembi kuti azionetsetsa kuti zonse zalembedwa bwino asanatumize mafomuwo.
◼ Ma CD Atsopano Omwe Alipo:
Live With Jehovah’s Day in Mind (cdjd)—Chingelezi, Chipwitikizi (ma CD 6)
◼ MP3 yatsopano yomwe ingakopedwe kuchoka pa www.pr418.com:
Live With Jehovah’s Day in Mind—Chingelezi (Amene ali ndi iPod angasankhe faelo ya M4B (AAC) imene ilinso ndi zithunzi za mutu uliwonse). Dziwani izi: Zinthu zimenezi si zoitanitsa. Ngakhale kuti gulu limalipira nthawi iliyonse imene munthu wakopera zimenezi, njira imeneyi ndi yosakwera mtengo kwambiri kuyerekeza ndi kupanga ndi kutumiza ma CD.