Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/08 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 12/08 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati anthu anena kuti ali ndi ana, agawireni buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. January 2009: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? February: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo.

◼ Gwiritsani ntchito mafomu mosamala. Pamakhala ntchito yambiri komanso pamafunika ndalama zochuluka pokonza mafomuwa. Nthawi zina kungakhale kofunikira kukumbutsa abale ena kuti mafomu a mpingo sayenera kugwiritsidwa ntchito polembapo zinthu zina ngakhale notsi. Mipingo ina imakhala ndi mapepala oti abale angalembepo zinthu zina m’malo mogwiritsa ntchito mafomu polemba zinthu zoterozo. Tikhozanso kupewa kuwononga mafomu ambiri mwa kukonza zimene talakwitsa pafomu osati kungotaya fomuyo. Ngakhale zili choncho onetsetsani kuti mafomu onse osungidwa m’mafaelo a mpingo komanso otumizidwa ku ofesi ya nthambi azikhala ooneka bwino komanso owerengeka bwino. Muyeneranso kusunga mafomu malo oyenerera oti asaphimbike ndi mafomu ena.

◼ Madisiki onse a MP3 a nyimbo zamalimba za Kingdom Melodies kuyambira pa voliyumu 1 kufika pa voliyumu imene yangotuluka kumene amatchedwa Kingdom Melodies—MP3. Tasiya kutumiza madisiki amenewa ndipo amene akufuna kukhala ndi nyimbozi angakopere pa Webusaiti yathu ya www.pr418.com. Ngakhale kuti gulu limalipira nthawi iliyonse imene munthu wakopera zimenezi, njira imeneyi ndi yosakwera mtengo kwambiri kuyerekeza ndi kupanga ndi kutumiza ma CD.

◼ Mabuku Atsopano Amene Alipo:

Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? (kt)—Chichewa, Chilomwe, Chingelezi (ndiponso Zilembo za Akhungu za Giredi 2), Chisena, Chiswahili, Chitonga (Malawi), Chitumbuka, ndi Chiyao.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena