Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu July ndi August: Ofalitsa angagwiritse ntchito kabuku kalikonse ka masamba 32 komwe ali nako pa timabuku totsatirati: Kodi Mulungu amatisamaliradi?, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha. September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? October: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Pa Msonkhano wa Utumiki womaliza musanapite ku msonkhano wachigawo, zabwerezeni malangizo ndi zofunika kukumbukira zimene zikukhudza mpingo wanu. Pakapita mwezi umodzi kapena iwiri mutachita msonkhano wachigawo, dzagwiritseni ntchito mbali ya zosowa za pampingo kukambirana mfundo za msonkhano wachigawo zimene ofalitsa aona kuti n’zothandiza muutumiki.
◼ Mwezi wa August ndi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa uli ndi masiku asanu a Loweruka ndiponso Lamlungu.