Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 28, 2009.
1. Kodi Akhristu masiku ano angagwiritse ntchito bwanji mfundo yopezeka pa Deuteronomo 14:1? [w05-CN 1/1 tsa. 28; w04-CN 9/15 tsa. 27 ndime 5]
2. Kodi mfundo ya pa Deuteronomo 20:5-7 ingagwire ntchito bwanji mumpingo wachikhristu masiku ano? [w04-CN 9/15 tsa. 27 ndime 6]
3. Kodi mtundu wa Isiraeli unali wosiyana motani ndi mitundu ina pankhani ya nkhondo? (Deut. 20:10-15, 19, 20; 21:10-13) [cl-CN mas. 134-135, ndime 17]
4. Kodi n’chiyani chingatithandize kutumikira Yehova mokondwera? (Deut. 28:47) [w95-CN 1/15 tsa. 16 ndime 4-5]
5. Kodi makolo angapindule motani ndi fanizo lopezeka pa Deuteronomo 32:9, 11, 12, limene limasonyeza mmene Yehova ankakondera Aisiraeli? [w01-CN 10/1 tsa. 9 ndime 7-9]
6. Kodi tiyenera kuwaona bwanji mawu osocheretsa amene Rahabi anauza amuna omwe anatumizidwa ndi mfumu kudzafufuza azondi? (Yos. 2:4, 5) [w93-CN 12/15 tsa. 25 ndime 1]
7. Kodi chitsanzo cha Aisiraeli chopezeka pa Yoswa 3:15, 16 chikutiphunzitsa chiyani? [w04-CN 12/1 tsa. 9 ndime 6]
8. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yoswa anachita Akani ataba? (Yos. 7:20-25) [w04-CN 12/1 tsa. 11 ndime 4]
9. Kodi lemba la Yoswa 9:22, 23, limasonyeza bwanji kuti zimene Mawu a Mulungu amanena zimachitikadi? [w04-CN 12/1 tsa. 11 ndime 3]
10. Kodi chitsanzo cha Kalebi chikutilimbikitsa motani? (Yos. 14:8, 10-12) [w04-CN 12/1 tsa. 12 ndime 2; w93-CN 5/15 tsa. 29 ndime 1]