Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tingatani kuti tizisunga nthawi pamisonkhano ya mpingo?
Nthawi sichedwa kutha tikamakambirana zinthu zosangalatsa. Pachifukwa chimenechi, nthawi zina zingakhale zovuta kukamba nkhani mogwirizana ndi nthawi imene tapatsidwa. Kodi chingatithandize n’chiyani kuthana ndi vutoli?
Yambani panthawi yake. Mpingo wonse ukasonkhana, zingakhale bwino kupempha omvera kuti akhale pansi kudakali mphindi imodzi kapena ziwiri pulogalamu isanayambe. Zikatere, msonkhano umayamba panthawi yake komanso mwadongosolo. (Mlal. 3:1) Misonkhano ya timagulu tochepa, monga misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda, isamayambe mochedwa poyembekezera obwera mochedwa.
Konzekerani bwinobwino. Chinsinsi chosungira nthawi ndi kukonzekera pasadakhale. Khalani ndi cholinga cha nkhani yanuyo m’maganizo. Dziwani mfundo zazikulu, ndipo zitsindikeni. Pewani kugogomezera mfundo zing’onozing’ono zosafunikira kwenikweni. Kambani nkhani yanu m’njira yosavuta kumva. Ngati nkhani yanu ili ndi zitsanzo kapena mbali yofunsa anthu ena mafunso, yesezani zimenezo. Ngati n’kotheka, mukamayeseza mokweza, tsimikizirani kuti nkhani yanu sikupitirira nthawi yake.
Gawani nkhani yanuyo. Kaya nkhani yanuyo ndi yokamba inu nokha kapena yokambirana ndi omvera, zingakhale bwino kuigawa zigawozigawo. Sankhani mphindi zimene mudzathera pachigawo chilichonse, ndipo lembani zimenezi m’mbali mwa notsi zanu. Ndiye pamene mukukamba, yang’anani nthawiyo kuti muone ngati mukuisunga. Pankhani yokambirana ndi omvera, pewani mtima wofuna kuti anthu apereke ndemanga zambiri kumayambiriro chifukwa zimenezi zingachititse kuti mukambirane mothamanga ndime zakutsogolo. Abale ochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ayenera kuonetsetsa kuti ali ndi nthawi yokwanira yokambirana bokosi la mafunso obwereza la kumapeto kwa phunzirolo. Afunikanso kusamala kuti asadye nthawi ya nyimbo ndi pemphero lomaliza.
Malizani panthawi yake. Misonkhano yomwe imakhala ndi mbali zingapo, monga Msonkhano wa Utumiki, wokamba nkhani aliyense ayenera kuonetsetsa kuti wayamba ndiponso kumaliza panthawi yake. Kodi mungatani ngati mwaona kuti abale ena adya nthawi? M’bale mmodzi kapena oposerapo angafupikitse nkhani zawo mwa kukamba mfundo zikuluzikulu zokha ndi kusiya mfundo zosafunikira kwenikweni kuti msonkhanowo uthebe panthawi yake. Ngati inu muli mphunzitsi waluso, mungathe kuchita zimenezi.
Ifeyo omvera, tingam’thandize kwambiri m’bale amene akuchititsa msonkhanowo ngati tipereka ndemanga zachidule koma zokhala mfundo zofunikira zokha. Chotero, tonsefe tingathandize kuti misonkhano izichitika “moyenera ndi mwadongosolo.”—1 Akor. 14:40.