Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamapanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, kuphatikizapo anthu amene anapezeka pa Chikumbutso kapena misonkhano ina koma sasonkhana nthawi zonse pamisonkhano ya mpingo, muyesetse kugawira buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. June: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena buku lina lililonse lomwe linatuluka chaka cha 1995 chisanafike.
◼ Kuyambira pano ndandanda ya msonkhano wachigawo sizipezekanso mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Koma nthawi zonse izipezeka mu Nsanja ya Olonda ya March 1. Choncho, akulu akulimbikitsidwa kuti azilengeza za masiku ndiponso malo a msonkhano amene mpingo wawo udzapite. Mutu wa msonkhano wachigawo 2010-2011 ndi wakuti “Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova.”
◼ Nkhani yapadera ya nyengo yachikumbutso cha 2010 ndi yakuti “Kodi Bata ndi Mtendere Weniweni Zidzakhalako Liti?”